Return   Facebook

The Universal House of Justice

Ridván 2024

To the Bahá’ís of the World

Dearly loved Friends,

Tsopano zaka ziwiri za ntchito yovuta zedi ya zaka zisanu ndi zinayi zatha. Abwenzi a Mulungu atengera pamtima kwambiri zolinga zake. Mu dziko lachiBahá’í monse pali kuzama kowonjezereka pa kumvetsetsa pa zomwe zikufunikira popitiliza kupititsa patsogolo ndondomeko yomanga dera ndi kusinthika kwa dera kwakukulu. Koma pakudutsa kwa tsiku lirilonse tikuona zinthu za m`dziko lapansi zikuvutira-vutira, kugawikana kukukulira-kulira. Mikangano yochuluka pakati pa anthu ndinso maiko ikukhudza anthu ndi malo munjira zochuluka.

Ichi chikusowekera yankho kuchokera kwa mzimu wina uliwonse wodalilika. Tonse tikuzindikira bwino lomwe kuti mbumba ya Dzina Lalikulu singayembekezere kukhala yosakhudzidwa ndi mavuto amenewa a dziko. Komabe, ngakhale ili yokhudzidwa ndi mavuto amenewa, sikuti yasokonezeka nawo; ndi yokhudzidwa ndi chisoni ndi kuvutika kwa mtundu wa anthu, koma sikuti yazingwa nawo. Kukhudzika kochokera pansi pamtima kuyenera kupangitsa kuchita kanthu mopitilira kumanga mbumba/madera amene angapereke chiyembekezo m`malo mwanjakata, kubweretsa umodzi pamene pali kukangana.

Shoghi Effendi anafotokoza momveka bwino momwe ndondomeko ya “kulowa pansi kopitilira kwa ntchito za anthu” ikuonekera molingana ndi ndondomeko ina, ndondomeko yolumikiza, nkudzera mwa iyo “Linga la chipulumutso cha munthu”, “pothawira pomaliza” pa dziko, likumangidwa. Ndife osangalala kuwona, mu dziko ndi chigawo china chilichonse, obweretsa mtendere owona ali otanganidwa ndi kumanga linga limeneli. Tikuona mu nkhani ina iliyonse mtima ukuyatsidwa ndi chikondi cha Mulungu, banja likutsegula khomo lake kwa abwenzi atsopano, ogwira ntchito limodzi akulunjika pa ziphunzitso za Bahá’u’lláh pofuna kuthana ndi mavuto a dera, mbumba imene ikulimbitsa khalidwe la kuthandizana, dera kapena mudzi ukuphunzira kuyambitsa ndi kupitiliza ntchito zofunikira pa kupita patsogolo kwake pauzimu ndinso kuthupi, dera likudalitsika ndi kukhazikitsidwa kwa Bungwe Lauzimu latsopano.

Njira ndi zida za Pulani zikuvomera mzimu wina uliwonse kusonkhera mbali ya chimene mtundu wa anthu ukufunika mu tsiku ili. Patali ndi kupereka thandizo la pompo lothetsa mavuto a nthawi yomweyo, ntchito za Pulani ndi njira imene ndondomeko zomanga za nthawi yayitali kudutsa mibadwo yochuluka zikukhadzikitsidwa dera lina lililonse. Zonsezi zikulunjika ku mathero osapeweka ndi a changu: Pakuyenera kukhala chiwerengero chachikulu, chopitilira cha iwo amene akupereka nthawi yawo, mphamvu zawo, ndi chidwi chawo ku chipambano cha ntchito imeneyi.

Ndi kutinso kwina, koma mu mfundo ya Bahá’u’lláh ya umodzi wa mtundu wa anthu, momwe dziko lapansi lingapeze masomphenya aakulu okwanira kuluzanitsa mbali zake zonse zosiyanasiyana? Angachite bwanjinso koposa kumasulira masomphenya amenewo mu dongosolo loyima pa umodzi mu kusiyana-siyana pomwe dziko lapansi lingachire ku mavuto a m’dziko amene aligawa ilo? Ndi ndani amene angakhale chotupitsa chimene kudzera mu icho anthu a dziko lapansi akhoza kupeza njira yatsopano ya moyo, njira yolunjika ku mtendere wosatha? Tambasulani choncho kwa wina aliyense dzanja la ubwenzi, la ntchito imodzi, la kutumikira kwapamodzi, la kuphunzira kwapamodzi, ndi kupita patsogolo ngati amodzi.

Tikuzindikira pamomwe kutaka-taka ndi mphamvu zikubwelera mu dera lina lililonse ndi achinyamata ake omwe akudzutsidwa ku masomphenya a Bahá’u’lláh ndikukhala atenga mbali a Pulani. Ndipo chomwecho, ndi kukoma mtima kozama, kulimba mtima ndi kudalira kotheratu pa Mulungu kumene achinyamata achiBahá’í ayenera kunyamuka ndi kufikira kwa amnzawo ndi kuwabweretsa mu ntchito iyi! Onse ayenera kusefukira, koma achinyamata akuyenera kutambasula mapiko awo ndi kuwuluka.

Changu cha ola ili chisatchinge chimwemwe chapadera chimene chimachokera mu kutumikira. Kuyitanidwa ku kutumikira ndi chinthu chokwezeka, chiyangato chachivomerezo. Kumakopa mzimu wokhulupirika uliwonse, ngakhale iyo imene ili yothodwa ndi zisamaliro ndi maudindo. Pakuti munjira zonse zimene mzimu wokhulupikawo watanganidwa nazo zitha kupezedwa mu kuzipereka kozama ndi kukhudzidwa kwa moyo wonse pa kuchita bwino kwa ena. Makhalidwe otere amapereka kukhala chikati-kati ku moyo wa zofuna zochuluka. Ndipo nthawi yotsekemera kwambiri pa zonse kwa mtima wina uliwonse woyatsidwa ndi imene umakhala limodzi ndi abale ndi alongo muuzimu, kutumikira ku zofunikira za dera limene likusowekera chakudya chauzimu.

Ku Malo Oyera, ndi mitima yosefukira, tikuthokoza Bahá’u’lláh pokudzutsani inu ndi kukuphunzitsani munjira Zake, ndipo tikupempha Iye kuti akutumizireni dalitso Lake.

 

Windows / Mac