Return   Facebook   Zip File

Obligatory

Ndichitira umboni, O Mulungu wanga, kuti Munandilenga ine, kuti ndikudziweni ndi kukupembedzani. Nditsimikizira, panthawi ino, kufooka kwanga ndi kukula kwa mphamvu Zanu, kusauka kwanga ndi kulemera Kwanu.

Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wothandiza pa Tsoka, Wodzidalira Nokha.

#13438
- Bahá'u'lláh

 

Iye amene afuna kunena Pempheroli, ayenera kuyimirira ndipo atembenukire kwa Mulungu, ndipo poimirira pamalo akewo, iye ayang’ane kudzanja lamanja ndi lamanzere, ngati kuti akuyembekezera chifundo cha Ambuye Wake, Wachifundo-Choposa, Womvera Chisoni. Tsono iye anene kuti:

O Inu Amene muli Ambuye wamaina onse ndi Mlengi wa miyamba! Ndikupemphani Inu kubzolera mwa iwo Amene ali kasupe a Uweniweni Wanu osaonekawo, Wokwezeka koposa, Waulemelero Onse, kuti mulipange pemphero langa, moto umene uwotche zophimba zimene zanditseka ine kuti ndisaone kukongola Kwanu, ndi kuwala kumene kunditsogolere ine ku nyanja ya kumene Inu Mukupezeka.

Kenaka iye akweze manja ake mopempha kulozera kwa Mulungu -wodalitsika ndi wokwezeka ndi Iye – ndipo anene:

O Inu Khumbo la dziko lapansi ndi Okondedwa wa amitundu! Inu mukundiwona ine ndikutembenukira kwa Inu, ndikudzilekanitsa kwa aliyense kupatula Inu, ndi kukakamira ku chingwe Chanu, chomwe kubzolera mu mayendedwe ake chilengedwe chonse chawongoleredwa.

Ndine mtumiki Wanu, O Ambuye wanga ndiponso mwana wa mtumiki Wanu. Onani ine ndili chilili kukonzekera kuchita Chifuniro Chanu ndiponso khumbo Lanu, ndi kusafuna china chilichonse kupatula chikondwerero Chanu chokoma. Ndikudandaulirani kubzolera m’nyanja ya chifundo Chanu ndi Nyenyezi ya Nthanda ya chisomo Chanu kuti muchite naye mtumiki Wanu monga momwe mufunira ndi kusangalatsidwira. Mwa nyonga zanu zomwe zili patali popitilira kutchula konse ndi chitamando chilichonse! Chimene chaululidwa ndi Inu ndikhumbo la mtima wanga ndiponso chokondedwa cha moyo wanga. "O Mulungu, Mulungu wanga! Musaone zimene ndifuna ndi zochita zanga koma muone chifuniro Chanu zimene zakutila kumwamba ndi pansi pano. Mu Dzina Lanu Lalikulu Lopambana kwambiri, O Inu Ambuye wa mafuko onse! Ndikufuna zokha zimene Inu mufuna, ndipo zokha zimene Inu Mukonda."

Kenaka iye agwade, ndikugwetsa mphumi yake pansi, anene kuti:

Okwezeka Muli Inu pamwamba pa chifotokozo cha wina aliyense kupatula Inu nokha, ndi kuzindikirika ndi kena kalikonse kupatula Inu.

Kenaka ayimilire ndi kunena:

“Pangani pemphero langa, O Ambuye wanga, mtsinje wa madzi a moyo pamene ndingathe kukhala moyo wautali monga m'mene ufumu Wanu ungakhalire, ndipo

ndingathe kutchula Inu mudziko liri lonse la Maiko Anu." Kenaka iye akwezenso manja ake mopempha, ndipo anene:

O Inu amene polekanitsidwa Nanu mitima ndi miyoyo yosungunuka, amenenso ndi moto wa chikondi Chake dziko lonse lapansi layatsidwa! Ndikudandaulira Inu mwa Dzina Lanu kubzolera mwa lomwe Inu mwagonjetsa chilengedwe chonse, musandimane ine chimene chilli ndi Inu, O Inu Amene mulamulira anthu onse! Inu mukumuona, O Ambuye wanga, mlendoyu kuthawira kwawo kokwezeka kopambana pansi pa chophimba cha ufumu Wanu, ndi cholengedwa chosaukachi kasupe wa chuma Chanu. Yanu ndi mphamvu yolamulira chilichonse chomwe Inu mufuna. Ndichitira umboni kuti Inu muyenera kutamandidwa mu zochita Zanu, ndi kukumverani mu chilamulo Chanu, ndi kukhalabe osakakamizidwa mu ulamuliro Wanu.

Kenaka a kweze manja ake ndi kunena Dzina Lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu.

Kenaka aweramire pansi manja ali pa maondo pamaso pa Mulungu – wodalitsika ndi okwezeka akhale Iye – ndi kunena:

Inu mukuona, O Mulungu wanga, momwe mzimu wanga wagwedezekera mkati mwa nthiti ndi ziwalo zanga, mkufunitsitsa kwake kuti ukupembedzeni Inu, ndi mkulakalaka kwake kuti ukukumbukireni Inu ndi kukulemekezani Inu; momwe ukuchitira umboni mu ufumu wa chinenero Chanu ndi kumwamba kwa Nzeru Zanu. Ndikonda mu khalidwe limeneli, O Ambuye wanga, kupempha kwa Inu zonse zimene muli nazo, kuti ndilangize umphawi wanga, ndi kukulitsa chaulere Chanu ndi chuma Chanu, ndi kulengeza kufooka kwanga, ndi kuvumbula mphamvu Zanu ndi Nyonga Zanu.

Kenaka iye ayimirire ndi kukweza manja ake kawiri mopempha, ndi kunena:

Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wamphamvu zonse, wachaulere Chonse. Kulibe Mulungu koma Inu, mkozi, poyamba ndi pomaliza pomwe. O Mulungu, Mulungu wanga! Chikhululuko Chanu chandilimbikitsa, ndipo kuyitana kwanu kwandidzutsa, ndipo chisomo chanu chandikweza ndi kunditsogolera kwa Inu. Ndine yani, kuti ndingathe kulimba mtima kuti ndiyimilire pachipata cha mzimu woyandikira Nanu, kapenanso kulodzetsa nkhope yanga ku nyali zomwe zili kuwala kuchokera kumwamba kwa chifuniro chanu? Inu mukuona, O Ambuye wanga, cholengedwa chochititsa chisonichi chikugogoda pakhomo lachisomo Chanu, ndi moyo wakuthawu ukufunafuna mtsinje wamoyo osatha kuchokera kumanja a chaulere Chanu. Chanu ndi chilamulo nthawi zonse, O Inu Amene muli Ambuye wa maina onse, ndipo kwanga ndi kusawiringula ndi kugonjera malolera ku chifuniro Chanu, O Mlengi wa miyamba!

Kenaka iye akweze manja ake katatu ndi kunena:

Wamkulu ndi Mulungu kuposa wamkulu aliyense!

Kenaka iye agwade ndi kugwetsa mphumi yake pansi, ndi kunena:

Muli apamwamba zedi Inu kukutamandani kwa iwo amene ali pafupi Nanu kuti afike kumwamba pafupi Nanu, kapena mbalame za mitima ya iwo amene ali odzipereka kwa Inu kuti afikedi pa chitseko cha chipata chanu. Ndichitira umboni kuti Muli opatulika pamwamba pa zizindikiro zonse, ndiponso Woyera pamwamba pa maina onse. Palibe Mulungu wina koma Inu, wopambana koposa onse, wa Ulemerero onse.

Kenaka akhazikike pansi ndi kunena:

Ndichitira umboni ku chimene zolengedwa zonse zachitira umboni, ndi makamu a kumwamba, ndi okhala mu Paradizo Okwezeka koposa, ndipo kuseri kwaoko lilime la ulemelero ili lomwe kuchokera ku malekezero a ulemelero onse, kuti Ndinu Mulungu, kuti kulibenso Mulungu koma Inu, ndipo kuti Iye Amene wavumbulutsidwa ndi chinsinsi chobisika, chizindikiro chosungidwa, kubzolera mwa Amene malembo B ndi E (kukhala) aphatikizana ndi kulukana pamodzi. Ndichitira umboni kuti ndi Iyeyo Amene dzina lake lalembedwa ndi Cholembera cha Wamwambamwamba, ndinso Amene watchulidwa mu Mabuku a Mulungu, Ambuye Wampando wa Chifumu m’mwambamo ndi pansi pano. Kenaka ayimilire njo ndi kunena:

O Ambuye wa zolengedwa zonse ndi mwini wa zinthu zonse zooneka ndi zosaoneka! Inu mukuiona misozi yanga ndi zisisimo zomwe ndikunena, ndi kumvetsera ku kubuula kwanga, ndi kuchema ndi chiliro cha mtima wanga. Ndi nyonga Zanu! Zolakwa zanga zanditsekerezera kumbuyo kuti ndisayandikire Nanu; ndipo machimo anga andiyimitsa kutali kuchokera kubwalo la milandu la chiyero Chanu. Chikondi Chanu, O Ambuye wanga, chandilemeza ine, ndipo malekano ndi Inu yandiononga ine, kutalikirana ndi Inu kwandidya ine.

Ndikupemphani Inu ndi mayendedwe Anu mu chipululuchi, ndiponso ndi mawu “Ndili pano, Ndili pano” amene osankhidwa Anu adalankhula mu ufumu Wanu, ndi mpumo wa Chibvumbulutso Chanu, ndi mphepo zodekha za kudza kwa Mbandakucha wa Mbvumbulutsi Wanu, kukonza kuti ndiyang’anire pa kukongola Kwanu ndi kutsata chilichonse chomwe chilli mu Bukhu Lanu.

Kenaka iye anene Dzina Lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu ndi kuweramira pansi manja ali pa maondo, ndi kunena:

Mayamiko akhale kwa Inu, O Mulungu wanga, pakuti Inu mwandithandiza kukumbukira Inu ndiponso kukuyamikani Inu, ndipo mwandizindikiritsa ine Iye Amene ali Mbandakucha wa Zizindikiro Zanu, ndipo mwandipangitsa kuweramira pansi pamaso pa Umbuye Wanu, ndi kudzichepetsa pamaso pa Umulungu Wanu, ndi kuvomereza chimene chayankhulidwa ndi lilime la ukulu wanu.

Kenaka iye aweramuke ndi kunena:

O Mulungu, Mulungu wanga! Msana wanga wawelama ndi kulemedwa kwa machimo anga, ndipo kusasamala kwanga kwandiononga ine. Ndikamaganizira kuipa kwa zochita zanga ndi chisamaliro Chanu, mtima wanga usungunuka mkati mwanga, ndipo magazi anga akuwira mkati mwa misempha yanga. Mwa kukongola Kwanu, O Inu khumbo la Dziko lapansi! Ndili ndi manyazi kukweza nkhope yanga kwa inu, ndipo manja anga olakalaka ali ndi manyazi kutambasukira kuloza kumwamba kwa chaulere Chanu. Inu mukuona, O Mulungu wanga, momwe misozi yanga ikundilepheretsa kukumbukira Inu ndi kukuza zabwino Zanu, O Inu Ambuye Wampando wa Chifumu m’mwambamo ndi dziko lapansi pano!

Ndikudandaulirani mwa zizindikiro za Ufumu Wanu ndi zodabwitsa za ulamuliro Wanu kuchita ndi okondedwa Wanu monga kuyenera chaulere Chanu, O Ambuye wa zamoyo zonse, ndipo muyeneradi chisomo Chanu, O Mfumu ya zooneka ndi zosaoneka!

Kenaka iye anene Dzina lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu ndi kugwada mphumi yake ili pansi ndi kunena:

Mayamiko akhale kwa Inu, O Mulungu wathu, pakuti Inu mwatitumizira ife chomwe chatisendeza m’fupi ndi Inu, ndipo mutipatse ife chabwino chilichonse chotumizidwa ndi Inu mu Mabukhu Anu ndi Malembo Anu. Titetezeni, tikupemphani Inu, O Ambuye wanga, ku makamu a malingaliro a zinthu zopanda pake, ndi maganizo achabe.

Inu, ndithudi, Ndinu Wanyonga, Wodziwa Zonse.

Kenaka awutse mutu wake ndikukhazikika pansi ndi kunena:

Ndichitira umboni, O Mulungu wanga, kuchimene osankhidwa Anu achichitira umboni, ndi kuvomereza chimene okhala ku Paradizo okwezekayo ndi iwo azinga mozungulira mpando Wanu Wamphamvu achivomereza. Maufumu adziko lapansi ndi kumwamba ndi Anu, O Ambuye wa maiko!

#13440
- Bahá'u'lláh

 

Amene akufuna kupempherayo, asambe manja ake, ndipo pamene ali kusamba, anene kuti:

Limbikitsani dzanja langa. O Mulungu wanga, kuti ligwire Bukhu Lanu ndi chilimbiko chomwe makamu a dziko lapansi sadzakhala ndi mphamvu kuligonjetsa. Litchinjirizeni tsono, kuti lisadudukire mchilichonse chomwe sichailo. Ndithudi, Inu muli Wanyonga, Wamphamvu Zopambana.

Ndipo pamene akusukusula nkhope yake iye anene kuti:

Ndatembenukira nkhope yanga kwa Inu, O Ambuye wanga! Iwalitseni ndi kuunika kwa nkhope Yanu. Itetezeni, chomwecho, posatembenukira kwa wina koma

Inu.

Tsopano ayimilire ndipo ayang’ane ku Qiblih (ku Bahji, Akka), iye anene kuti:

Mulungu achitira umboni kuti kulibe Mulungu wina koma Iye. Maufumu a Chibumbulutso ndi chilengedwe ndi Ake. Iye, muchoonadi, wabvumbulutsa Iye Amene adayankhula pa Sinai, amene kubzolera mwa Iye Dangaliro lopambana lawalitsidwa, ndipo Mtengo wa Loti umene paseri pake palibe podzera wayankhula, ndipo kubzolera mwa Iye chiitano chalengezedwa kwa onse amene ali m’mwamba ndi padziko lapansi: “Taonani Mwinizonse wabwera. Dziko lapansi ndi kumwamba, ulemelero ndi ulamuliro ndi wa Mulungu, Ambuye wa anthu onse, ndi Mwini wa za m’mwambamo ndi pansi pano!”

Tsopano Iye, aweramira pansi, manja ali pa maondo ndi kunena kuti:

Wokwezeka Ndinu pamwamba pa chitamando changa ndi chitamado cha wina aliyense pambali panga, opitirira chifotokozo changa ndi chifotokozo cha onse amene ali kumwamba ndi onse amene ali pa dziko lapansi!

Tsopano iye ayimirire atatambasula manja ake zikato zitapenya kumwamba molunjika nkhope, ndi kunena kuti:

Musamukhumudwitse, O Mulungu wanga, Iye amene, ndi zala zodandaula, wakakamira ku mpindiro wa chifundo Chanu ndi chisomo Chanu, O Inu Amene mwa iwo amene alangiza Chifundo Chopambana!

Ndipo iye akhazikike pansi, ndi kunena kuti:

Ndichitira umboni ku umodzi Wanu ndi chiphatikizo Chanu, ndi kuti Inu Mulungu, ndipo kuti kulibenso Mulungu wina pambali Panu, Inu, ndithudi, mwaulula Chipembedzo Chanu, mwakwaniritsa Pangano Lanu, ndi kutsegulitsa chitseko cha chisomo Chanu kwa onse amene akhala kumwamba ndi dziko lapansi. Dalitso la mtendere, malonje ndi ulemelero, zikhale pa okondedwa Anu, amene zosintha ndiponso mwayi wa dziko lapansi sizidawalepheretse kutembenukira kwa Inu, ndipo amene adapereka zawo zonse, m’chiyembekezo chokapeza chijacho chimene chilli ndi Inu. Inu zedi, muli Wokhululukira-khululukirabe, Wachaulere Chonse.

(Ndipo ngati wina aliyense atasankha m’malo mwa ndime yayitali atangonena mawu awa: “Mulungu achitira umboni kuti kulibe Mulungu wina koma Iye, Wothandiza Patsoka, Wodzidalira Yekha,” ndipokwanira. Chimodzimodzi ndipokwaniranso ngati iyeyo atakhazikika pansi asankhe kunena mawu awa: “Ndichitira umboni ku umodzi Wanu ndi chiphatikizo Chanu, ndipo kuti Inu Ndinu Mulungu, ndi kuti kulibe

Mulungu wina pambali Panu.”)

#13439
- Bahá'u'lláh

 

General

ANA

O Ambuye wanga! Pangani kukongola Kwanu kukhale chakudya changa, ndikupezeka Kwanu ndi chakumwa changa ndipo chitamando Chanu ndiye kuchita kwanga ndipo kukumbukira Inu ndiye mzanga, ndipo mphamvu ya Ulumuliro Wanu ndi chithandizo changa, malo Amene Mukhala ndi ku khomo kwanga, ndipo malo anga omwe ndikhala ndi malo omwe inu mwawadalitsa kuchokera ku muyeso umene mwaupereka kwa iwo amene azitsekera poziphimba kwa inu. Inu ndinu, ndithudi, wamkulu, wa ulemelero onse, wamphamvu zonse.”

#13449
- Bahá'u'lláh

 

O Inu a Chifundo Ambuye! Ndine mwana wamng’ono, ndikwezeni ine pondilora ine ku ufumu. Ndili wa dziko lapansi, ndipangeni ndikhale wakumwamba, ine ndili wotsika padziko, ndiloleni ine ndikhale wa maiko am’mwamba; mdima, ndifuteni ine kuti ndikhale woyera; chinthu cha dziko ndipangeni ine wauzimu, ndipo ndipatseni kuti ndi bvumbulutse mphatso Zanu zopanda malire. Inu ndinu Wamphamvu, Wachikondi Chonse.

#13450
- Bahá'u'lláh

 

O Mulungu wanga, Okondedwa wanga, khumbo la mtima wanga.

#13446
- The Báb

 

O Mulungu! Lelani kakhanda aka pa chifungatiro chachikondi Chanu, ndipo mukapatse mkaka wochokera kumaere a Mphatso Yanu. Samalirani kachomeraka m’munda wamaluwa wa chikondi Chanu ndikukathandiza kukula kubzolera mumbvumbi wa chaulere Chanu. Kapangeni kukhala kamwana ka Ufumu ndipo katsogozeni kumwamba Kwanu. Inu Ndinu wamphamvu ndi wokoma mtima, ndipo Inu Ndinu Wopatsa, Wosamana, Ambuye a chaulere chopambana.

#13447
- `Abdu'l-Bahá

 

O Mulungu! Phunzitsani ana awa. Ana awa ali zomera za m’munda Wanu wazipatso, maluwa a M’dimba Lanu, Lozesi wa m’munda Wanu. Lolani kuti mvula Yanu iwagwere; lolani kuti dzuwa la choonadi liwalire pa iwo ndi chikondi Chanu. Lolani kuti mweya Wanu uwatsitsimutse mwakuti iwo aphunzitsidwe, akule ndipo adzadziwe, ndi kuoneka okongola kweni-kweni. Inu Ndinu Wopatsa. Inu Ndinu Wachisoni.

#13448
- `Abdu'l-Bahá

 

O Ambuye anga! O Ambuye anga! Ine ndine mwana wa zaka zochepa. Ndidyetseni ine kuchokera ku mawere a chifundo Chanu, ndipangeni ine kukhala muchifungatiro chachikondi Chanu, ndiphunzitseni ine musukulu ya chitsogozo Chanu ndipo mundipambanitse ine pansi pa nthunzi wa mphatso Yanu. Ndilanditseni ine kuchokera mu mdima, ndipangeni ine kukhala kuwala konyezimira; ndichotsereni ine kusakondwa, ndipangeni ine kukhala duwa m’munda wa lozesi, ndiwalitseni ine kukhala wantchito pakhomo Lanu loyera ndipo perekani kwa ine makhalidwe a umunthu ndi chilengedwe cha chiyero; ndipangeni ine chiyambi cha mphatso kwa wanthu adziko lapansi ndipo vekani mutu wanga ndi chisoti cha moyo wosatha. Indetu, Inu ndinu Wamphamvu, Wamkulu, Woona, Wakumva.”

#13451
- `Abdu'l-Bahá

 

ANYAMATA

O Ambuye! Muwalitseni mnyamatayu ndipo mupatseni wolengedwa wosakayu chaulere Chanu. M’ninkheni iye nzeru, mupatseni mphamvu zoonjezereka pakucha pa m’mawa uliwonse ndipo msungeni mkati mwatchinga la chitetezo Chanu mwakuti apulumutsidwe ku zolakwa, achirimike pakutumikira ntchito Yanu, alangize osokera, atsogoze okhumudwa, amasule a m’ndende ndikudzutsa onyalanyaza, kuti onse adalitsidwe ndi chikumbukiro ndi chitamando Chanu. Inu Ndinu Wamphamvu ndi Wanyonga.

#13452
- `Abdu'l-Bahá

 

BUNGWE LA UZIMU

Pamene mulowa mchipinda chokumanira, nenani pemphero ili ndi mtima wogunda ndi chikondi cha Mulungu ndi lirime loyeretsedwa kuzonse koma chikumbukiro Chake, kuti Wamphamvu Zonseyo mwachifundo Akuthandizeni kupeza chipambano chachikulu:

O Mulungu, Mulungu wanga! Ife tili antchito Anu amene tatembenukira modzipereka kunkhope Yanu yoyera, amene tadzilekanitsa tokha kuzinthu zonse kupatula Inu pa Tsiku loyera-yerali. Ife tasonkhana mu

Bungwe la Uzimu ili, wogwirizana m’malingaliro athu ndi m’maganizo athu, ndi mzolinga zathu zobvomerezana kukweza Mau Anu pakati pa anthu. O Ambuye, Mulungu wathu! Tipangeni ife kukhala zizindikiro za Chitsogozo Chanu choyera, mbendera za Chikhulupiliro Chanu chokwezeka pakati pa anthu, antchito kuchipangano

Chanu champhamvu, O Inu Ambuye wathu wam’mwambamwamba, abvumbulutsi a umodzi Wanu Woyera mu ufumu Wanu wa Abha, ndi nyenyezi zowala zowunikira maiko onse.

Ambuye! Tithandizeni ife kuti tikhale nyanja zoyendetsedwa ndi mafunde a chisomo Chanu chodabwitsa, mitsinje yoyenda kuchokera kumitundu Yanu yoyera-yera, zipatso zabwino pa mtengo wa chiphunzitso Chanu cha kumwamba, mitengo yogwedezedwa ndi mphepo ya Chaulere Chanu m’munda Wanu wakumwamba. O Mulungu! Pangani mizimu yathu kutsamira pa malemba a Umodzi Wanu woyera, mitima yathu kukondweretsedwa ndi m’bvumbi wa chisomo Chanu, kuti tigwirizane ngati mafunde a m’nyanja imodzi ndikulumikizana ngati Malawi akuwala Kwanu kwakukulu; kuti maganizo athu, malingaliro athu, kumva kwathu kukhale ngati choona chimodzi, kusonyeza mzimu wa umodzi kubzolera mdziko lonse lapansi. Ndinu wa Chisomo, wa Chaulere, Wopatsa, wa Mphamvu Zonse, wa Chifundo, Wachisoni.

#13453
- `Abdu'l-Bahá

 

Pemphero lonenedwa potseka msonkhano wa Bungwe Lauzimu.

O Mulungu! O Mulungu! Kuchokera ku ufumu wosaoneka wa umodzi Wanu tioneni ife tasonkhana mu msokhano wa uzimuwu, kukhulupirira mwa Inu, kukhulupirira zizindikiro Zanu, wolimba mu Pangano ndi Mawu Anu, okopedwa kwa Inu, tiyatseni ife ndi moto wa chikondi Chanu ndi kukhukupirika ku Chipembedzo Chanu.

Ndife antchito m'munda Wanu, ofalitsa Chipembedzo Chanu, okhulupirika okupembedzani Inu, odzichepetsa kwa okondedwa Anu, odzitsitsa pa chitseko Chanu, ndipo tikukupemphani Inu kutilimbikitsa ife potumikira osankhika Anu, kutithandiza ife ndi makamu Anu osaoneka, kutilimbikitsa ife mukutumikira ndi kutipanga ife odzipereka ndi okonda kuyankhula ndi Inu.

O Ambuye athu! Ndife ofooka, ndipo Inu ndi Wamphamvu, Wanyonga. Ndife opanda moyo, ndipo Inu Mzimu wopereka moyo, Ndife osowa, ndipo Inu ndi Wokwaniritsidwa, Wamphamvu.

O Ambuye athu! Tembenuzirani nkhope zathu ku Chifundo Chanu, tidyetseni ife kuchokera ku gome la Kumwamba Kwanu ndi Chisomo Chanu chosefukira, tithandizeni ife ndi makamu a angelo Anu ndi kutilimbikitsa ife kupyolera mwa oyera a mu Ufumu wa Abhá.

Indetu, Inu Ndinu Wopatsa, Wachifundo. Inu Ndinu Mwini wa Mphatso zonse, ndipo, indetu, Inu Ndinu Wachisoni ndi wa Chisomo.

#13454
- `Abdu'l-Bahá

 

CHIKHULULUKIRO

O Inu Wamphamvu zonse! Ine ndine wochimwa, koma Inu Ndinu Wokhululukira! Ine ndiri wosakwanira, koma Inu muli wachisoni! Inde ndiri mumdima wa uchimo koma Inu Ndinu nyali ya Chikhululukiro! O Inu Mulungu Wachifundo! Khululukirani machimo anga, ndipatseni mphatso Zanu, iwalani mphulupulu zanga, ndichinjirizeni ndi kundimiza m’kasupe wa chipiliro Chanu ndipo ndichizeni ine kudwala konse ndi matenda.

Ndiyeretseni ndi kundidalitsa ndipo ndipatseni gawo kuchokera ku mbvumbi wakuyera, mwakuti chisoni ndi kusakondwa zichoke ndipo chisangalalo ndi chimwemwe zitsike. Lolani kuti nkhawa ndi makaiko zisanduke kukondwa ndi kukhulupirira ndipo bvomerani kuti kulimba mtima kulowe m’malo mwa mantha.

Ndithudi, Inu Ndinu Wokhululukira, Wachisoni, ndipo Ndinu Waufumu ndi Wokondeka.

#13455
- `Abdu'l-Bahá

 

CHITETEZO

O Ambuye wanga! Inu Mudziwa kuti wanthu azunguliridwa ndi zowawa ndi matsoka ndipo adzazidwa ndi zolemetsa ndi mabvuto. Yeso lirilonse limtsata munthu ndipo chobvuta chilichonse chikumlonda ngati kuluma kwa njoka. Palibe tchinga ndi pothawira kwa iye koma pansi pa phiko la chitetezo, kusamala, kulonda ndi kusunga Kwanu.

O Inu Wachifundo, O Ambuye wanga! Konzani chitetezo Chanu chikhale chida changa, kusamala Kwanu chishango changa kudzichepetsa pakhomo la umodzi Wanu mlonda wanga, ndikusunga Kwanu ndikutchinga Kwanu linga langa ndipokhala panga. Ndisamalireni ine ku maganizo anga ndi zofuna zanga ndipo Ndilanditseni ku matenda, mayesero, mabvuto ndi masautso. Ndithudi, Inu Ndinu Mtetezi, Mchinjirizi, Msungi, Wokwaniritsa, ndipo ndithudi, Inu Ndinu Wachifundo wa achifundo Chopambana.

#13456
- `Abdu'l-Bahá

 

CHITHANDIZO

O Mulungu wanga! Ndikupemphani, kubzolera mdzina Lanu la Ulemelero, kundithandiza mu zimene zingapange ntchito za atumiki Anu kupita patsogolo, ndikukulitsa mizinda Yanu. Inu indetu, muli ndi mphamvu pazinthu zonse!

#13457
- Bahá'u'lláh

 

Ambuye! Ife ndife womvetsa chisoni, tipatseni chifundo Chanu; ndife wosauka, tipatseni gawo kuchokera ku nyanja ya chuma Chanu; ndife wosowa, tikwaniritseni; wosayenera, tipatseni ulemelero Wanu. Mbalame zamlengalenga ndi nyama za mu thengo zimalandira zakudya zawo tsiku ndi tsiku kuchokera kwa Inu ndipo za moyo zonse zimalandira chisamaliro ndi chikondi Chanu. Musam’mane wofookayu chisomo Chanu chodabwitsa ndipo gwetselani mwa mphamvu Yanu madalitso Anu akulu pamzimu wobvutikawu.

Tipatseni ife chakudya chathu chalero ndi zofunikira za moyo wathu, kuti tisadalire pa aliyense koma Inu Nokha, tigwirizane kotheratu ndi Inu, tiyende munjira zanu ndi kuwuza anthu za kudabwitsa Kwanu. Inu Ndinu Wamkulu ndi Wachikondi ndi amene Mupereka kwa mtundu wonse wa anthu.

#13458
- `Abdu'l-Bahá

 

CHITSOGOZO

O Mulungu! O Mulungu! Timwetseni ife kuchokera mchikho cha chaulere Chanu. Walitsani nkhope zathu ndi nyali yachitsogozo. Tilimbikitseni ife mkukhulupirika ndi kulimbikira m’chipangano Chanu cha nkhalakale. Tiloleni tikhale antchito Anu woongoka. Tsegulani pamaso pathu zitseko zachuma, tikonzereni ife njira zopezera umoyo, tipatseni mkate kupyolera m’njira zimene ife tiribe nazo ulamuliro m’chuma Chanu chakumwamba! Tipatseni mphamvu kuti tipenyetse maso athu kunkhope Yanu yachifundo ndikukhala wokhulupirika m’chiphunzitso Chanu.

O Inu Wachifundo ndi Wachisoni! Ndithudi, Inu ndinu Wachisomo kwa amene ali chilili ndi kulimbika mu Pangano Lanu lolimba ndi losagwedezeka. Atamandike, Ambuye wa maiko onse.

#13459
- `Abdu'l-Bahá

 

O Mulungu, nditsogozeni, nditetezeni, ndipangeni kukhala nyali yowala ndi nyenyezi yonyezimira. Inu Ndinu wamkulu ndi wamphamvu.

#13460
- `Abdu'l-Bahá

 

KUCHIRITSA

Dzina Lanu ndilo kuchira kwanga, O Mulungu wanga, ndipo kukumbukira Inu ndi mankhwala anga. Kuyandikira kwa Inu ndi chiyembekezo changa, ndipo kukonda Inu ndibwenzi langa. Chifundo Chanu kwa ine ndikuchitira kwanga ndi chithandizo changa m’dziko lino ndi mdziko liri nkudza. Inu, ndithudi, Ndinu wa chaulere chonse, Wodziwa Zonse, Wanzeru Zonse.

#13461
- Bahá'u'lláh

 

Ulemerero ukhale kwa Inu, O Mbuye Mulungu wanga! Ndikupemphani Inu m'dzina Lanu. kupyolera mmene Iye Amene Ndiye kukongola Kwanu, wakhazikitsidwa pa ufumu wa Chipembedzo Chanu, ndipo ndi m'dzina Lanu kupyolera m'lomwero musintha zinthu zonse ndipo musonkhanitsa zinthu zonse pamodzi, ndi kuitana zinthu zonse ku bwalo ndikusupa zinthu zonse, ndi kuteteza zinthu zonse. Ndikupemphani Inu kulondera mdzakaziyu amene wathawira ku mpumulo Wanu ndipo wafunafuna mthunzi wa Amene mwa Iye Inu mwaonekeramo ndipo waika chikhulupiriro ndi chigomezero chake chonse mwa Inu.

Mdzakaziyu akudwala, O Mulungu wanga ndipo walowa kunsi kwa mthunzi wa Mtengo wa machiritso Anu, wokanthidwa, ndipo wathawira ku Mzinda wa chitetezo Chanu, wadwala, ndipo wafunafuna Mutu wa Kasupe wa kukoma mtima Kwanu; wobuwula ndi ululu, ndipo wakangazira kuti akapeze Chitsime cha Mweza wa kudekha Kwanu; walemedwa ndi tchimo, ndipo walunjikitsa nkhope yake ku bwalo la chikhululukiro Chanu.

Muvekeni iye, mwa ulamuliro Wanu ndiponso mwa chikondi cha kukoma mtima Kwanu, O Mulungu wanga ndi Wokondedwa wanga, ndi chovala cha chitonthozo ndi kuchiritsa Kwanu, ndipo mpangeni iye kumwera mu chikho cha chifundo ndi kukoma mtima Kwanu.

Mtetezeni iye, makamaka ku zovuta ndi zopweteka zonse, ku zowawa zonse ndi matenda ndiponso kuchokera ku chiri chonse choyipa kwa Inu.

Inu, m'chowonadi, Muli Wokwezeka kopambana pamwamba pa zonse kupatula Inu Mwini. Inu indetu, Ndinu Wochiza, Wokwaniritsa Zonse, Msungi, Wokhululukira, Wachifundo chopambana.

#13462
- Bahá'u'lláh

 

KUDZIPATULA

O Ambuye wanga, wokondedwa wanga, khumbo langa! Khalani bwenzi langa pamene ndili ndekha ndikundiperekeza Ine pamene ndathamangitsidwa kuchoka kwathu. Chotseleni chisoni changa. Ndipangeni kuti ndikhale wodzipereka kukukongola kwanu. Ndibwezeni kwa aliyense koma Inu Nokha. Ndikopeni kubzolera mkununkhira kwanu koyera. Ndipangeni kuti ndichezerane mu ufumu Wanu ndi iwo amene adzipatula ku zinthu zonse koma Inu Nokha, amene afunitsitsa kutumikira ku khomo Lanu lopatulika ndikuima kugwira ntchito mchiphunzitso Chanu. Ndipangeni ndikhale m’modzi wa adzakazi Anu amene afika ku chikondwerero Chanu. Indetu, Inu Ndinu Wachisomo, Wachaulere.

#13463
- `Abdu'l-Bahá

 

O Ambuye wanga Wolemekezeka! Ndithandizeni kuleka malingaliro osayenera; kugonjetsa chilakolako chonse cholusa, kuyeretsa zofuna-funa za makhalidwe anga; kudzitengera ndekha kufatsa kumene chipongwe chilichonse sichingakusokoneze; kuchipiliro chimene zowawa sizingachigwedeze; kukhulupirika kumene zofuna za mtima wanga sizingakusunthe; kuti ndikhale woyenera kukutumikirani Inu ndi kuphunzitsa Mau Anu.

#13464
- `Abdu'l-Bahá

 

KUDZIPEREKA

Mulungu pangeni kukhala bango la Mphako, mmene thima la kudzikonda lakolokotedwamo, tsono kuti ndi khale mphako yoyera mmene chikondi Chanu chingadutsire popita kwa ena. Ndasiya mbuyo mwanga kusadekha ndi kusakhutira. Ndidzipereka ndekha kwa thunthu mmanja Mwanu, pakuti Ndinu Chitsogozo Changa mchipalamba, Mphunzitsi wa umbuli wanga. Sing'anga wa nthenda yanga. Ndine msilikali mgulu la nkhondo la Mfumu yanga, ndapereka chifuniro changa kwa Iye ndi moyo wanga-kuti Achite nawo mmene Iye Afunira. Sindidziwa tsogolo ndi lotani mwandikonzera ine, ndiponso sindifuna kufufunza kapena kufuna kudziwa. Tchito m'tsiku indikwanira ndipo tsogolo lonse liri Lanu.

Pang'ono ndi pang'ono Inu musintha kufooka kukhala nyonga, kukaika kukhala kukhulupirira, kusokonezeka kukhala kumvetsetsa. Pomwe ndi oyenera kusenza chipsinjo, Inu Muchiyedzeka pa phewa langa. Pamene ndakonzeka kulowa m'thengo, Inu Mundipatsa malo m’gulu la nkhondo la kuwala. Tsopano ndiribe ntchito ina yoposa kumvala zirimbe muntchito Yanu. Ndi kufunitsitsa ndiponso kudekha, ndi chiyembekezo ndiponso kuthokoza ndi weramira ku ntchito ya ora lino, kuopa kuti; pamene kuitana Kwanu kudza ndingapezeke osakonzeka.

#13465
- `Abdu'l-Bahá

 

KULIMBIKIRA

O Ambuye Mulungu Wanga! Thandizani wokondedwa Anu kukhala wolimba m’chikhulupiliro chanu, kuyenda munjira Zanu, ndikukhala wochilimika mu ntchito Yanu. Apatseni chisomo Chanu kuti athe kulimbana ndi zilakolako zawo, kutsata kuwala kwa chitsogozo chauzimu. Inu Ndinu Wamphamvu, Wachisomo, Wodzidalira Nokha, Wopereka Madalitso, Wachikondi, Wamkulu, Wachaulere Chonse.

#13466
- `Abdu'l-Bahá

 

KUPHUNZITSA

O Mulungu! O Mulungu! Ino ndi mbalame yothyoka phiko ndipo kuwuluka kwake ndi kwapang’onopang’ono, ithandizeni kuti ithe kuwuluka kufika kunsonga ya chuma ndi chipulumutso, iwuluke ulendo wake ndi chimwemwe ndi chisangalaro chonse kunka mu mlengalenga mopanda malire, kwezani nyimbo yake m’Dzina Lanu Lalikulu mu zigawo zonse, sangalatsani makutu ndi kuyitanaku, ndikuwalitsa maso pakuwona zizindikiro za chitsogozo!

O Ambuye! Ndine m’modzi, ndekha, ndi wopepuka. Kwa ine kulibe mtsamiro wina uliwonse koma Inu Nokha, ndilibe mthandizi Ndinu Nokha ndipo ndilibe mtonthozi wina woposa Inu. Ndilimbikitseni mu ntchito Yanu, ndithandizeni kulankhula za nzeru Zanu pakati pa zolengedwa Zanu. Indetu, Inu Ndinu mthandizi wa ofooka ndi mtchinjirizi wa ang’onoang’ono, ndipo indetu, Inu Ndinu Wamphamvu, Wamkulu ndi Wosakakamizidwa!

#13467
- `Abdu'l-Bahá

 

O Inu Mulungu Wosafaniziridwa! O Inu Ambuye wa Ufumu! Miyoyo iyi ndi ankhondo Anu akumwamba. Athandizeni iwo, ndipo ndi magulu Akhamu Lapamwamba Muwapambanitse; kuti yense wa iwo akhale ngati gulu la nkhondo ndi kugonjetsa maikowa kupyolera mu chikondi cha Mulungu ndi kuwala kwa uzimu kwa Chiphunzitso Chanu.

O Mulungu! Mukhale wowatchinjiriza ndi Mthandizi wao, ndipo m’chipululu, m’phiri, m’chigwa, m’nkhalango, m’madambo ndi m’nyanja, khalani Inu wowasangalatsa – kuti alire kupyolera mu mphamvu ya Ufumu ndi kuuzira kwa Mzimu Woyera!

Indetu, Inu Ndinu Wamphamvu, Wamkulu ndi Mwinimphamvu, ndiponso Inu Ndinu Wanzeru, Wakumva ndi Woona.

#13468
- `Abdu'l-Bahá

 

O Mulungu wanga! O Mulungu wanga! Inu mukundiona ine mukutsika kwanga ndi kufooka kwanga, otanganidwa ndi ntchito yaikulu, ndikutsimikiza kukweza liwu Lanu pakati pa magulu a wanthu ndi kufalitsa ziphunzitso Zanu pakati pa anthu Anu. Ndingapambane bwanji popanda kuthandizidwa ndi Inu ndi kuuzira kwa Mzimu Woyera, ndithandizeni kuti ndipambane ndi makamu a ufumu Wanu wa ulumerero. Ndikundipatsa chitsimikizo Chanu chimene pachokha chikhoza kusintha kachilombo kakang’ono kwambiri koluma kukhala chiombankhanga, kadontho ka madzi kukhala mitsinje ndi nyanja ndipo kanthu kakang’ono kukhala kuwala ndi dzuwa?

Inu ndinu Wamphamvu ndi Wochita chilichonse chimene mufuna.

#13469
- `Abdu'l-Bahá

 

KUSALA KUDYA

Mayamiko akhale kwa Inu, O Ambuye Mulungu wanga! Ndikupemphani Inu mwa Chibvumbulutso chomwechi chimene chasandutsa m’dima kukhala kuwala, kubzolera muchomwechi Kachisi Wanu wobwerezedwa10 bwerezedwa wamangidwa, ndipo Uthenga Wolembedwa waululidwa, ndi Kalata Yolalikidwa yamasulidwa kunditumizira ine ndi iwo amene ali ndi ine chimene chingatithandize kuuluka kunka kumwamba kwa ulemelero Wanu wopambana, ndikutitsuka ife litsilo la kusakhulupilira lomwe lalepheretsa okaika kulowa mu Kachisi wa umodzi Wanu.

Ine ndine, O Ambuye wanga, amene ndagwira molimba chingwe chachikondi Chanu, ndikukakamirira ku mpindiro wa chisomo ndi chifundo Chanu. Ndikonzereni ine pamodzi ndi okondedwa anga zabwino zadziko lino ndi zadziko limene liri m’kudza. Agawireni iwo, tsono mphatso Zobisika zimene Munawakonzera osankhidwa pakati pazolengedwa Zanu.

Tsono awa, O Ambuye wanga, ndimasiku amene mwawalamulira a ntchito Anu kusala kudya. Ngodala iye amene asala chakudya chifukwa cha Inu Nokha ndikudzipatula kotheratu kuzinthu zonse koma Inu Nokha. Ndithandizeni ine ndikuwathandiza iwo, O Ambuye wanga, kubvera Inu ndi kusunga malamulo Anu.

Inu, indetu, Muli ndi mphamvu yochita zomwe Mwasankha. Kulibe Mulungu wina koma Inu Nokha, Wodziwa zonse. Mayamiko onse akhale kwa Mulungu, Ambuye wa maiko onse.

#13445
- Bahá'u'lláh

 

KUYAMIKA

Likuzike Dzina Lanu, O Ambuye Mulungu wanga! Inu ndi Iye amene zinthu zonse zimpembedza ndi Amene sapembedza kanthu. Amene Ali Ambuye wa zinthu zonse ndipo Sali kapolo wa kanthu. Amene Adziwa zonse koma sadziwidwa ndi kanthu. Inu Munafuna kuzizindikiritsa Nokha kwa wanthu; choncho, kupyolera mwa liu lapakamwa panu munadzetsa chilengedwe ndi kupanga m’mwamba. Palibe Mulungu wina koma Inu Nokha, Mkozi, Mulengi, Wamkulukulu, Wamphamvu Zonse.

Ndikupemphani, mwa liu lomweli, limene lawala pamwamba pa mzere wa Chifuniro Chanu, mundilore ndimwe mokwanira, madzi amoyo amene mwatsitsimutsa nawo mitima ya wosankhidwa Anu ndi kuukitsa mizimu ya wokondedwa Anu, kuti ine nthawi zonse, m’zooneka zonse, nditembenukire nkhope yanga kwa Inu.

Inu Ndinu Mulungu Wamphamvu, Waulemelero ndi Chaulere. Kulibe Mulungu wina pambali Panu, Woweruza Wamkulu, Woyerayera, Wanzeru-zonse.

#13470
- Bahá'u'lláh

 

M’BANDAKUCHA

O Mulungu wanga ndi Mbuye wanga! Ine ndine wantchito Wanu, ndi mwana wantchito Wanu. Ndadzuka pamphasa panga m’bandakucha uno pamene nthanda ya umodzi wanu yaunikira kuchokera m’bandakucha wa chifuniro Chanu, ndipo kuunika kwake kwakwanira padziko lonse lapansi, monga momwe kunalonjezedwera mu Mabuku a Chilamulo Chanu.

Matamando akhale kwa Inu. O Mulungu Wanga, Kuti tadzuka kuulemelero ndi kuona kuwala kwa Nzeru Zanu. Tumizani pansi pano, tsono, kwa ife, O Ambuye wanga, chomwe chidzatipanga ife kusiya aliyense koma Inu, chomwe chidzatichotsera kumangika ndi kalikonse, koma Inu Nokha. Ndilembereninso ine, pamodzi ndi iwo amene ali okondedwa anga, ndi abale anga, amuna ndi akazi omwe, zabwino zadziko lino ndi za dziko liri mkudza. Tisamalireni, tsono, kubzolera mu chitetezo Chanu chosalephera, O Inu Wokondedwa wa chilengedwe chonse ndi khumbo la miyamba yonse, kuchokera kwa iwo amene munawapanga kukhala cholowa cha iye wonong’ona zoipa, amene anong’ona m’mitima ya anthu. Muli ndi mphamvu kuchita monga momwe mufunira. Indetu, Ndinu Wamphamvu zonse, Wothandiza pa tsoka, Wodzidalira Nokha.

Dalitsaninso, O Ambuye Mulungu wanga, Iye amene Inu munamuika pamwamba pa maudindo Anu akulu, amene kubzolera mwa Iye, Inu mwasiyanitsa pakati pa anthu a umulungu ndi oipa, ndipo mwachisomo tithandizeni kuchita zomwe Inu muzikonda ndi kuzifuna. Adalitseni Inu, koposetsa, O Mulungu wanga, iwo amene ali Mau anu ndi Malemba Anu, ndi iwo amene aika nkhope zao kwa Inu, ndikutembenukira ku nkhope Yanu, ndikumvera kuitana kwanu. Inu, ndithudi, Ndinu Mbuye ndi Mfumu ya anthu onse, ndipo muli wamphamvu pa zinthu zonse.

#13441
- Bahá'u'lláh

 

M’MAWA

Ndauka mu chifungatiro Chanu, O Mulungu wanga, ndipo ndikoyenera kwa iye wofuna chifungatirocho kukhalamo mu Malo Oyera a chitetezo Chanu ndi mu Tchinga la linga Lanu. Walitsani m’kati mwanga, O Ambuye wanga, ndikuwala kwa m’bandakucha wa Chibvumbulutso Chanu, monga momwe mudawalitsa thupi langa ndi kuwala kwa m’mawa wa chaulele Chanu.

#13442
- Bahá'u'lláh

 

MADZULO

O Mulungu wanga, Mbuye wanga, mathero Achofuna changa, uyu, wantchito Wanu, afuna kugona mum’thunzi wa chifundo Chanu, ndikupumula pansi pa chifungatira cha chisomo Chanu, akupempha chisamaliro Chanu ndi chitetezo Chanu.

Ine ndikupemphani Inu, O Ambuye wanga, kuti ndi diso Lanu limene siligona, mulonde maso anga kuti asayang’ane china pambali pa Inu. Limbikitsani, choncho masomphenya ake kuti aone zizindikiro Zanu, ndikuyang’ana ku mzere wa Chibvumbulutso Chanu. Inu ndinu amene patsogolo pa zibvumbulutso za ukulu Wanu, maonekedwe amphamvu agwedezeka.

Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wamphamvu Zonse, Wogonjetsa Onse, Wosakakamizidwa.

#13443
- Bahá'u'lláh

 

O ofufuza Choonadi! Ngati ukukhumba kuti Mulungu atsegule maso ako, uyenera kupempha kwa Mulungu, kupemphera ndi kuyankhula Naye pakati pausiku, ndi kunena:

O Ambuye, Ndatembenuzira nkhope yanga ku ufumu

Wanu wa umodzi ndi kudzimiza m’nyanja ya chifundo Chanu. O Ambuye, walitsani maso anga powona kuwala Kwanu pakati pa usiku uno, ndi kundipanga kukhala osangalala ndi vinyo wa chikondi Chanu mu m’badwo wopambanawu. O Ambuye, ndipangeni kuti ndimve kuitana Kwanu, ndipo tsengulani pamaso anga zitseko zakumwamba Kwanu, choncho kuti ndiwone kuwala kwa ulemerero Wanu ndi kukopedwa ndi kukongola Kwanu.

Indetu, Inu ndi Wopatsa, Woolowamanja, Wachifundo, Wokhululukira.

#13444
- `Abdu'l-Bahá

 

MANJA A NTCHITO YA MULUNGU

Kuwala ndi ulemelero, malonje ndi mayamiko zikhale pa Manja a Ntchito Yake amene kupyolera mwa iwo nyali yobvutika nthawi – yaitali, yawala, ndi kukhazikitsidwa kwa udindo kunazindikirika kuti nkuchokera kwa Mulungu, Wamphamvu, Wamkulu, Wapayekha ndi kupyolera mwa omwe nyanja yopatsa iyendayenda, ndi mphepo ya chifundo cha Mulungu, Ambuye wa anthu onse, yauziridwa. Ife tipempha mwa Iye – wam’mwamba Ndiye – kuti awachinjirize iwo ndi magulu Ake, kuwayang’anira ndi ufumu Wake, ndi kuwathandiza ndi mphamvu Zake zomwe zagonjetsa zinthu zonse, Ufumu ndi wa Mulungu, Wolenga za kumwamba, ndi Mfumu wa Ufumu wa Maina onse.

#13471
- Bahá'u'lláh

 

MSONKHANO

Inu Ambuye wachifundo! Awa ndi antchito Anu amene akumana mu msonkhano uno, atembenukira ku ufumu Wanu ndipo akusoweka mpatso ndi madalitso Anu. O Inu Mulungu! Mvumbulutsani ndi kuwonetsa zizindikiro za umodzi Wanu zimene zaikidwa mu za moyo zonse.

Mvumbulutsani ndi kuwonetsa makhalidwe amene Inu mwawaika mwa anthuwa. O Mulungu! Ife tili monga zomera, ndipo mphatso Yanu ili monga mvula; tsitsimutsani ndi kupanga zomerazi kukula kupyolera mu mphatso Zanu. Ife ndi antchito Anu; tipulumutseni ku zinthu za dziko. Ndife mbuli; tipangeni kukhala ozindikira. Ndife akufa; tipangeni tikhale a moyo. Ndife okonda zinthu zopanda pake; tipatseni mzimu. Ndife omanidwa; tipangeni tikhale olandila zodabwitsa Zanu. Ndife osowa; tilemeletseni ndi kutidalitsa kuchokera ku chuma Chanu chopanda malire.

O Mulungu! Titsitsimutseni ife, tipatseni ife maso; tipatseni ife makutu; tidzazeni ife ndi zodabwitsa zamoyo, choncho kuti zobisika za ufumu Wanu ziwululidwe ndipo tidzikhuthule ku umodzi Wanu. Mphatso iliyonse imachokera kwa Inu; pemphero lirilonse ndi Lanu.

Inu ndinu Wanyonga. Inu Ndinu Wamphamvu. Inu Ndinu Wopatsa, ndipo Inu ndi Wachaulere nthawi zonse.

#13472
- `Abdu'l-Bahá

 

MTUNDU WA ANTHU

O Ambuye Wachisoni! Inu Amene Muli Wopatsa ndi Wachifundo! Ife tiri woperekera zikho pakhomo lanu ndipo tiri pansi pa chitetezo cha chifundo Chanu. Dzuwa la ubwino Wanu likuwalira pa onse, ndipo mitambo ya chifundo Chanu iphimba onse. Mphatso Zanu zizungulira onse, ubwino Wanu uli ndi mphamvu yochotsa zonse; chitetezo Chanu chiphimba onse, maonekedwe a zabwino Zanu awalira onse.

O Ambuye! Tipatseni ife zaulere Zanu zosatha ndipo lolani kuti nyali ya chitsogozo Chanu iwale. Walitsani maso athu, sangalatsani miyoyo yathu ndipo perekani mzimu watsopano m’mitima yonse. Tipatseni moyo wosatha. Tsegulani zitseko za nzeru Zanu; lolani nyali ya chikhulupiliro iwale. Lumikizani ndi kubweretsa anthu onse pansi pa m’thunzi umodzi, kunsi kwa mbendera ya chitetezo Chanu, kuti akhale ogwirizana ngati mafunde a nyanja imodzi, ngati masamba ndi nthambi za mtengo umodzi, asonkhane pansi pa chithuzi-thuzi cha hema imodzi. Aloleni kuti amwe pa kasupe m’modzi. Atsitsimutsidwe ndi mvumbi umodzi. Alandire kuwala kochokera kumalo amodzi a nyali ndi moyo. Inu ndinu wopatsa, wachifundo.

#13473
- `Abdu'l-Bahá

 

OMWALIRA

Ulemelero ukhale kwa Inu, O Ambuye Mulungu wanga! Musanyasidwe naye iye amene Inu mwamkweza kupyolera mu mphamvu ya ufumu Wanu wamuyaya, ndi kumsiya kutali ndi Inu, amene Inu Munamlola kulowa m’chihema Chanu cha kunthawi zosatha. Kodi Mungamtaye, O Mulungu wanga iye amene Inu Mwamphimba ndi Ufumu Wanu ndipo mungamtembenukire, O chifuniro changa amene Mwakhala pothawira pake? Mungamunyoze iye amene Inu Mwamtukula, kapena Kumuiwala iye amene Inu munanthandiza kukukumbukirani? Wolemekezedwa, kwamtheradi Muli Wolemekezedwa Inu! Inu muli Amene kuyambira pachiyambi Mwakhala Mfumu ya chilengedwe chonse ndi Woyendetsa Wake ndipo mpaka ku nthawi zosatha Mudzakhalabe Ambuye wa zolengedwa zonse ndi Mkozi Wake.

Wolemekezedwa muli Inu, O Mulungu wanga! Ngati Muleka kuchitira chisoni antchito Anu, ndani nanga angawachitire chisoni? Ndipo ngati Mukana kudyetsa okondedwa Anu, kuli ndaninso woti angawadyetse? Wolemekezedwa, kwamtheradi Muli Wolemekezedwa

Inu! Inu Mulambiridwa m’choonadi Chanu, ndipo Inu ndithudi ife tonse tikupembedzani, ndipo Inu Muli woonekera m’chilungamo Chanu, ndipo kwa Inu tonse, ndithu tichitira umboni. Inu muli, mchoonadi, wokondedwa mchisomo Chanu. Palibe Mulungu wina koma Inu Wothandiza pa Tsoka, Wosasowa kanthu.

#13474
- Bahá'u'lláh

 

Iye ndi Mulungu, ndi Iye Wokwezeka, Ambuye wokoma mtima ndi wa chaulere! Ulemelero ukhale kwa Inu, O Inu Mulungu wanga, Ambuye Mwini-mphamvu.

Ine ndichitira umboni ku Umwini-mphamvu Wanu, Ukulu Wanu, Ufumu Wanu, Kukomamtima Kwanu, Chisomo Chanu ndi Mphamvu Yanu, Umulungu Wanu, umodzi wa khalidwe Lanu, kupatulika Kwanu ndi kukwezeka Kwanu pamwamba padziko la chilengedwe ndi zonse ziri m’menemo.

O Mulungu wanga, Mukundiona ine ndadzipatula kuzinthu zonse koma kwa Inu, ndakakamira kwa Inu ndi kutembenukira kunyanja ya mphatso Zanu, kumwamba kwa chaulere Chanu, ku Nthanda ya Chisomo Chanu.

Ambuye! Ine ndichitira umboni kuti mwa wantchito Wanuyu munaikamo cholowa Chanu, ndiwo mzimu umene Inu Munapatsa nawo moyo kudziko lapansi.

Ndikupemphani kupyolera kwa Chibvumbulutso Chanu, mwa chifundo Chanu. Bvomerani zimene iye wazichita bwino m’masiku Anu. Mloleni chomwecho kuti abvekedwe ndi ulemelero wa ubwino Wanu ndi kuwalitsidwa ndi kulandilidwa Kwanu.

O Ambuye wanga, ineyo ndi zolengedwa zonse tichitira umboni kumphamvu Zanu ndi kukupemphani kuti musausiye mzimu uwu kutali ndi Inu umene wakwera kwa Inu, kumalo Anu akumwamba, ku Paradiso Wanu wokwezeka ndikumpumulo wofupikira kwa Inu.

O Inu amene Muli Ambuye wa anthu onse! Lolani tsono, O Mulungu wanga, kuti wantchito Wanuyu achezerane ndi osankhika Anu, Oyera Anu ndi Atumiki Anu m’malo a kumwamba amene cholembera sichingathe kunena kapena lilime kusimba.

O Ambuye wanga, wosaukayo wathamangiradi ku Ufumu wa chuma Chanu, mlendoyu wafika kwao mkati mwa mabwalo Anu, iye waludzu ku mtsinje wakumwamba wa chaulere Chanu. Musam’mane, O Ambuye gawo lake la phwando la chisomo Chanu ndi Chifundo cha chaulere Chanu. Inu zoonadi Ndinu Wamphamvu-zonse, Wachisomo, Wachaulere!

O Mulungu wanga cholowa Chanu chabwezedwa kwa Inu. Nkoyenera chisomo Chanu ndi chaulere Chanu zimene zazungulira ulamuliro Wanu mdziko lapansi ndi kumwamba, kupereka kwa yemwe Mwamlandira tsopanoyu mphatso Zanu ndi madalitso Anu, ndi zipatso za mtengo wa chisomo Chanu! Muli ndi mphamvu kuchita monga momwe Mufunira. Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wachisomo, Wachaulere chodzaza, Wachisoni, Wopatsa, Wokhululukira,

Wamtengowapatali, Wodziwa-zonse.

Ndichitira umboni, O Ambuye wanga, kuti Inu Mwawafunsa anthu kulemekeza mlendo wao, ndipo yemwe wakwera kwa Inu wafikadi kwa Inu ndipo walandiridwa pamaso Panu. Chitanayeni chomwecho malinga ndi chisomo Chanu ndi chaulere Chanu! Mwaulemerelo Wanu, Ine ndidziwa kwa mtheradi kuti simudzakana chimene Inu mwawalamulira akapolo Anu kapena simudzam’mana iye amene wakakamira pa chingwe cha chaulere Chanu ndi kukwera ku kasupe wa chuma Chanu.

Kulibe Mulungu wina koma Inu, M,modzi Yekha, Wamphamvu, Waponse-ponse, Wachaulere.

#13475
- Bahá'u'lláh

 

(Pempheroli liyenera kugwiritsidwa kwa a Bahá’í okha amene ali ndi zaka zoyambila “Ndi pemphero lokhali lokakamiza la chiBahá’í limene limanenedwa pa gulu; liyenera kunenedwa ndi modzi mwa okhulupilira pamene onse abwerapo atayima…” –Kitáb-I-Aqdas)

O Mulungu wanga! Uyu ndi mtumiki Wanu ndi mwana wa mtumiki Wanu amene anakhulupirira Inu ndi zizindikiro Zanu, ndi kutembenukira nkhope yake kwa Inu, ndi kudzipatula kotheratu ku zonse koma Inu Nokha.

Inu zowonadi Ndinu mwa amene awonetsa chifundo wa chifundo chonse. Chitanayeni, O Inu Amene Mukhululukira machimo a anthu ndi kukwirira zoyipa zawo, monga momwe kufunikira m’mwamba mwa chaulere Chanu ndi nyanja ya chisomo Chanu. Mulowetseni kumalo a chifundo Chanu chachikulu amene analipo asanakhale maziko apansi ndi kumwamba. Kulibe Mulungu wina koma Inu Nokha, Wokhululukira Nthawi Zonse, wa Chaulere Chonse.

Onena pempheroli anene:

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tipembedza Mulungu (19)

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tigwada pamaso pa Mulungu (19)

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tili wodzipereka kwa Mulungu (19)

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tiyamika Mulungu (19)

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tithokoza Mulungu (19)

“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)

Ife tonse, indetu, tili ndi chipiriro mwa Mulungu (19)

Bahá’u’lláh

(Ngati womwalira ali mkazi, wonena pemphero anene: Uyu ndi mdzakazi Wanu ndi mwana wa mdzakazi Wanu………)

O Mulungu wanga! O Inu wokhululukira machimo, Wopereka mphatso, Wochotsa masautso! Indetu, ndikupemphani kukhululukira machimo a iwo amene asiya mayala a thupi ndi kukwera kudziko lauzimu.

O Mbuye wanga! Ayeretseni ku zoipa, achotsereni chisoni, ndipo sandulizani mdima wawo ukhale kuwala. Apangeni kulowa mmunda wa chimwemwe, atsukeni ndi madzi woyerayera, ndipo aloleni kuti awone kuwala Kwanu paphiri lalitali koposa.

#13476
- `Abdu'l-Bahá

 

PANGANO

O Mulungu, Mulungu wanga! Atchingireni atumiki Anu wokhulupirika ku zoyipa za kudzikonda ndi dama, atetezeni ndi kulondera kwa diso la chikondi Chanu ku zopinga zonse, udani ndi dumbo, asungeni mlinga lolimba la chisamaliro Chanu ndipo, asakhale wokayika, apangeni kukhala zitsanzo za zizindikiro za ulemerero Wanu, walitsani nkhope zawo ndi kuwala kopambana kochokera ku m’bandakucha wa umodzi Wanu wa uzimu, sangalatsani mitima yawo ndi malemba omwe aululidwa kuchokera mu ufumu Wanu woyera, limbikitsani mafupa awo ndi mphamvu zanu zokokolora zodzera kumwamba kwa ulemerero Wanu. Inu Ndinu wa Chaulere Chonse, Mtetezi, Wamkulu, Wachisomo.

#13477
- `Abdu'l-Bahá

 

PHWANDO LA MASIKU 19

O Mulungu! Chotsani izo zonse zoyambitsa kusagwirizana, ndipo tikonzereni ife tonse izo zimene zili zoyambitsa umodzi ndi mgwirizano! O Mulungu! Tsitsani pa ife kununkhira kwa kumwamba! Tipatseni ife zotipindulitsa zonse ndi chakudya chonse. Tikonzereni ife chakudya cha chikondi! Tipatseni ife chakudya chanzeru! Tipatseni chakudya chowalitsidwa cha kumwamba!

#13482
- `Abdu'l-Bahá

 

UKWATI

Ulemelero ukhale kwa Inu, O Mulungu wanga! Indetu, wantchito Wanuyu ndi mdzakazi Wanuyu asonkhana pansi pa m’thunzi wa chifundo Chanu ndipo agwirizana kubzolera muchifundo ndi kuolowa manja Kwanu. O Ambuye! Athandizeni iwo m’dziko Lanu lino ndi Muufumu Wanu ndipo akonzeleni iwo zabwino zonse kubzolera mu chaulere ndi chisomo Chanu.

O Ambuye! Alimbikitseni iwo mkukutumikirani ndipo athandizeni mu ntchito Yanu. Muwapange iwo kukhala zizindikiro za Dzina Lanu mdziko Lanu ndipo atetezeni iwo kubzolera mu mphatso Zanu zimene siziguga mu dziko lino ndi mu dziko lirinkudza. O Ambuye! Iwo akupempha ku Ufumu wa chifundo Chanu ndi kuyitana ku ufumu wa Nokha Wanu.

Indedi, akwatirana pakumvera lamulo Lanu. Apangeni iwo kukhala zizindikiro za kumvana ndi umodzi kufikira kutha kwa nthawi. Indedi Inu Ndinu Wanyonga Zonse, Waponseponse ndi Wamphamvu Zonse!

#13483
- `Abdu'l-Bahá

 

ULENDO

Ndadzuka m’mawa uno ndi chisomo Chanu, O Mulungu wanga, ndikunyamuka pakhomo panga ndi kukhulupirira kotheratu mwa Inu, ndi kudzipereka ndekha ku chisamaliro Chanu. Tumizani tsono, pa ine, kuchokera ku mwamba kwa chifundo Chanu, madalitso ochokera kwa Inu, ndipo Mundilole ndibwerere kwathu bwino monga momwe Munandilolera kunyamuka muchitetezo Chanu, ndi maganizo anga onse ali pa Inu. Kulibe Mulungu wina koma Inu Nokha, M’modzi Yekha, Wosafanizilika, Wodziwa Zonse, Wanzeru Zonse.

#13484
- Bahá'u'lláh

 

O Mulungu, Mulungu wanga! Ndanyamuka pa khomo langa, kugwiritsitsa chingwe cha chikondi Chanu, ndipo ndadzipereka ndekha kwathuthu ku chisamaliro Chanu ndi chitetezo Chanu. Ndikupemphani Inu ndi mphamvu Yanu imene Inu mwateteza nayo okondedwa Anu ku zopinga ndi makhalidwe oipa, ndi kwa ankhanza ndi achiwembu amene akhala kutali ndi Inu, nditetezeni ine ndi mphatso Zanu ndi chisomo Chanu. Ndiloleni, tsono, ndibwerere kwathu ndi mphamvu Zanu ndi nyonga Zanu.

Inu, Choonadi, Wamphamvu Zonse, Wothandiza pa Tsoka, Wodzidalira Nokha.

#13485
- Bahá'u'lláh

 

UMODZI

O Mulungu wanga! O Mulungu wanga! Lumikizani mitima ya antchito Anu, ndipo Muwaululire iwo cholinga Chanu Chachikulu. Aloleni iwo atsate malangizo Anu ndi kusunga malamulo Anu. Athandizeni iwo, O Mulungu, mukuyesetsa kwao, ndipo muwapatse mphamvu kuti akutumikireni Inu. O Mulungu, Musawasiye iwo mwa iwo okha, koma mutsogoze mapazi awo ndi kuwala kwa nzeru Zanu ndipo sangalatsani mitima yawo ndi chikondi Chanu. Indetu, Inu Ndinu Mthandizi wawo ndi Mbuye wawo.

#13486
- Bahá'u'lláh

 

Mulungu lolani kuti kuwala kwa mgwirizano kukutire dziko lonse lapansi, ndi chizindikiro chakuti “Ufumu ngwa Mulungu” chisindikizidwe pamphumi pa anthu Ake onse.

#13487
- Bahá'u'lláh

 

Ulemelero ukhale kwa Inu, O Mulungu, chifukwa chakuwonetsa chikondi Chanu kwa mtundu wa anthu! O Inu Amene Muli Moyo wathu ndi Kuwunika kwathu, tsogolereni a ntchito Anu mu njira Yanu, ndipo mutipatse kukhala wolemera mwa Inu ndi kukhala omasuka ku ziri zonse kupatula Inu Nokha.

O Mulungu, Tiphunzitseni Umodzi Wanu ndipo Mutipatse kuzindikira Mgwirizano Wanu, kuti tisawone aliyense koma Inu Nokha. Inu Ndinu Wachifundo ndi Wopatsa Chaulere. O Mulungu, Lengani m’mitima ya wokondeka Anu moto wa chikondi Chanu, kuti utenthe maganizo a chirichonse kupatula a Inu Nokha.

Tiululireni, O Mulungu, Ukulu Wanu wosatha-kuti Inu mudalipo ndipo mudzakhalapobe nthawi zonse, ndipo kuti kulibenso Mulungu wina koma Inu Nokha. Indetu, mwa Inu tidzapeza chitonthozo ndi mphamvu.

#13488
- Bahá'u'lláh

 

WOCHOTSA MASAUTSO

55. O Inu amene mayesero Ake ndi mankhwala ochiritsa kwa iwo amene ali pafupi Nanu, lupanga Lake liri chifuniro chopambana cha onse amene akukondani Inu, mubvi Wake ndi pempho lapamtima la mitima ya iwo amene akuzindikira choonadi Chanu! Ndikupemphani, mwa kukoma Kwanu kwa uzimu ndi kunyezimira kwa ulemelero wa nkhope Yanu, kuti Mutitumizire ife kuchokera ku malo Anu m’mwamba chimene chingatipangitse ife kuyandikira kwa Inu.

Choncho Limbikitsani mapazi athu, O Mulungu wanga M’Chiphunzitso Chanu, ndipo Walitsani mitima yathu ndi kuwala kwa nzeru Zanu, ndipo Unikirani m’zifuwa zathu ndi kuunika kwa Maina Anu.

#13491
- Bahá'u'lláh

 

Kodi palinso wina Wochotsa masautso kupatula Mulungu? Nenani: Atamandike Mulungu! Iye Ndiye Mulungu! Onse ndi antchito Ake ndipo onse akhala mu ulamuliro Wake!

#13489
- The Báb

 

54. Tinene: Mulungu Akwaniritsa zinthu zonse pamwamba pa zinthu zonse, ndipo kulibe chilichonse kumwamba kapena m’dziko lapansi koma Mulungu Akwaniritsa. Indetu, Iye Ali mwa Iye Mwini Wodziwa, Wosasowakathu, Mwinimphamvu.

#13490
- The Báb

 

Iye ndi Wachisoni, Wachaulere Chonse! O Mulungu,

Mulungu wanga! Inu mukundiwona ine, Inu mukundidziwa ine; Inu amene muli Panthunzi panga ndi

Pothawira panga, Palibe amene ndasankha kapena kufufuza kupatula Inu, palibe njira yomwe ine ndayendamo kapena kufuna kudzayenda koma mnjira Yanu ya chikondi Chanu.

Mu mdima wa ndiwe yani wa mabvuto, maso anga amatembenukira ndi oyembekezo ndi odzadzidwa ndi chikhulupiriro ku m'mawa wa chifundo Chanu chopanda malire ndipo ora la m’bandakucha mzimu wanga wofoka umatsitsitmutsidwa ndi kulimbikitsidwa pokumbukira kukongola Kwanu ndi ungwiro Wanu. Iye amene chisomo cha chifundo Chake chamuthandiza, ngakhale kuti katakhala kadontho kakang’ono, kadzasanduka nyanja yopanda malire, ndipo kanthu kochepetsetsa kamene kathandizidwa ndi chifundo Chake, kadzawala ngati nyenyezi lowalitsitsa.”

“Khalani pansi pa chitetezo Changa, O Mzimu Wanga wa chiyero, Inu amene muli Opereka Zaulere Zonse, wantchito Wanu uyu wokondedwa ndi, wowalitsidwa. Muthandizeni mu dziko ili la umunthu kuti akhale osagwedezeka ndi olimba mu chikondi Chanu ndipo mpatseni iye amene ali mbalame yothyoka phiko kuti apeze pothawira ndi mthuzi wa chisa Chanu cha uzimu chimene chakhazikika pa mtengo wa kumwamba.”

#13492
- `Abdu'l-Bahá

 

YODALITSIKA NDIYO MBUTO

Yodalitsika ndiyo mbuto, ndi nyumba, ndi malo, ndi mzinda, ndi mtima, ndi phiri, ndi pothawira, ndi phanga, ndi chigwa, ndi mtunda, ndi nyanja, ndi chilumba, ndi dambo, kumene dzina la Mulungu latchulidwako, ndi chitamando Chake chalemekedwako.

#13493
- Bahá'u'lláh

 

ZOYENERA MU UZIMU

Nenani: O Mulungu, Mulungu wanga! Bvekani mutu wanga ndi chisoti cha chilungamo, ndipo kongoletsani nkhope yanga ndi mchitidwe woongoka. Inu indetu, Ndinu Mwini mphatso ndi zaulere zonse.

#13495
- Bahá'u'lláh

 

O Mulungu! Tsitsimutsani ndi kusangalatsa mzimu wanga. Yeretsani mtima wanga. Walitsani mphamvu zanga. Ndikupereka zanga zonse m’dzanja Lanu. Inu ndiye Chitsogozo changa ndi Pothawira panga. Sindidzakhala wachisoni ndi wokhumudwa; Ndidzakhala munthu wokondwa ndi wosangalala. O Mulungu! Sindidzakhalanso ndi nkhawa, kapena kulola mabvuto kundigonjetsa. Sindidzakhala pa zinthu zosakondweretsa moyo.

O Mulungu! Inu Ndinu bwenzi langa kwa ine kuposa m’mene ndiri ine kwa ine mwini. Ndikudzipereka kwa Inu, O Ambuye.

#13496
- `Abdu'l-Bahá

 

O Ambuye! Ndife wofooka; tilimbikitseni. O Mulungu! Ndife mbuli; tipangeni kukhala wozindikira. O Ambuye! Ndife amphawi; tipangeni kukhala wolemera. O Mulungu! Ndife akufa; titsitsimutseni. O Ambuye! Ndife wosayenerezeka konse; tipatseni ulemerero mu ufumu Wanu. Ngati mutithandiza, O Ambuye, tidzakhala ngati nyenyezi zothwanima. Ngati simutithandiza, tidzakhala wotsika kuposa dziko lapansi limene.

O Ambuye! Tilimbikitseni. O Mulungu! Tipatseni kupambana. O Mulungu! Tithandizeni kugonjetsa kudzikonda ndi chilakolako. O Ambuye! Tipulumutseni ku nsinga za dziko lapansi. O Ambuye! Titsitsimutseni kupyolera mu kuuzira kwa Mzimu Woyera kuti tsono tithe kuchilimika ndi kukutumikirani, kukupembedzani, ndikudzipereka kwa thunthu mu ufumu Wanu ndi chikhulupiriro chonse.

O Ambuye! Inu Ndinu Wamphamvu! O Mulungu, Inu

Ndinu Wokhululukira! O Ambuye, Inu Ndinu

Wosamalira!

#13497
- `Abdu'l-Bahá

 

Occasional

ZOPEREKA KUTHUMBA

Abwenzi onse a Mulungu …… ayenera kusonkha monga momwe angathere, chingakhale pang’ono chabe. Mulungu sakakamiza aliyense kupambana zomwe ali nazo. Zosonkhazi ziyenera kuchokera ku madera ali onse ndi kwa wokhulupirira aliyense …..

O abwenzi a Mulungu! Khulupirani motsimikiza kuti mmalo mwa zoperekazi, minda yanu, mafakitale anu, ndi mabizinesi anu adzadalitsika kwakukulu, ndi mphatso zokoma ndi chaulere. Iye amene abwera ndi ntchito yabwino kamodzi adzalandira mphotho kakhumi. Palibe kukayika kuti Ambuye wamoyo adzalimbikitsa mowirikiza iwo amene agwiritsa ntchito chuma chawo mu njira Yake.

O Mulungu, Mulungu wanga! Walitsani zikope za wokondeka Anu oona ndipo muwathandize ndi makamu a angelo mkupambana kosapeneka. Limbikitsani mapazi awo mu njira Yanu yowongoka, ndipo kuchokera ku chaulere Chanu chakalekale atsekulireni makomo amadalitso Anu; chifukwa akugwiritsa ntchito chuma chawo munjira Yanu yomwe Inu Mudawapatsa, kuchinjiriza Chikhulupiliro Chanu, kuyika chikhulupiliro chawo m’kukumbukira Inu, ndi kusagwiritsitsa chomwe ali nacho chifukwa cha kupembedza Kukongola Kwanu ndi kufunafuna kwawo njira zokusangalatsirani Inu.

O Ambuye wanga! Agawireni gawo lawo lopambana, mphatso yosankhidwa ndi malipiro osakayikira. Ndithudi, Inu Ndinu Mchinjirizi, Mthandizi, Osaumira, Wachaulere, Wopatsa Nthawi Zonse.

#13494
- `Abdu'l-Bahá

 

Tablets

PEMPHERO LA AHMAD

Iye Ndiye Mfumu, Wodziwa zonse, Wanzeru!

Taonani, Mbalame ya M’Paradiso iyimba pa nthambi za Mtengo Wamuyaya, ndi nyimbo zoyera ndi zokoma, kulalikira kwa woona mtima thenga wabwino wa kuyandikira kwa Mulungu kuwaitanira okhulupilira mu Umodzi wa Uzimu kubwalo la Pamaso pa Wopatsayo, kuwauza anthu wotsatira za uthenga womwe wabvumbulutsidwa ndi Mulungu, Mfumu, Waulemerero, Wopanda mzake, kuwatsogolera okondedwa kumpando wopatulika ndi kwa wokongola konyezimirayu.

Indetu, Uyu ndi Wokongola Kopambana amene ananenedwa m’mabukhu a Atumwi, kupyolera mwa amene choonadi chidzalekanitsidwa ndi chonama ndipo nzeru ya lamulo lirilonse idzayesedwa. Indetu, Iye Ndiye Mtengo wa Moyo umene umabweretsa zipatso za Mulungu, Wokwezeka, Wamphamvu, Wamkulu.

O Ahmad! Chitirani umboni kuti ndithudi Iye Ndiye Mulungu ndipo palibe Mulungu koma Iye, Mfumu, Mtetezi, Wosafanizidwa, Mwini Mphamvu. Amene Iye

Wamtuma m’dzina loti Ali (Bábu Woyera) anali Woona wodzera kwa Mulungu Amene Malamulo Ake tonse tibvomereza.

Nenani: O wanthu inu khalani omvera malangizo a Mulungu amene alembedwa mu Bayani ndi wa Ulemereloyo, Wanzeru. Ndithudi, Iye ndi Mfumu ya Atumwi ndipo Bukhu Lake ndi Mai wa Mabukhu mukadadziwa.

Chomwecho Mbalame ikuitana inu kuchokera mu ndende iyi. Iye Ayenera kupereka uthenga womvekawu. Kwa iye amene safuna aukane uphunguwu ndi kwa iye amene afuna asankhe njira yopita kwa Ambuye ake. O anthu inu, ngati mukana mau awa, mwakhulupilira mwa Mulungu ndi chitsimikizo chotani? Tiwonetseni, O gulu la wabodza. Ai, mwa M’modzi Amene asunga moyo wanga m’dzanja Lake sangathe ndipo sadzatha kuchita izi ngakhale atagwirizana kuthandizana wina ndi mzake.

O Ahmad! Musaiwale mphatso Zanga pamene Ine palibe.

Kumbukirani masiku Anga m’masiku a moyo wanu ndi masautso Anga ndi kumangidwa Kwanga m’ndende iyi yakutali. Ndipo khalani wolimbika m’chikondi Changa kuti mtima wanu usagwedezeke, ngakhale malupanga a adani akukang’antheni ndi kumwamba konse ndi dziko zikuukileni. Khalani monga lawi la moto kwa adani Anga ndi mtsinje wa moyo wosatha kwa wokondedwa Anga, ndipo musakhale a iwo wokaika. Ndipo mukakumana ndi zosautsa m’njira Yanga kapena kunyazitsidwa chifukwa cha Ine, musabvutike nazo.

Tsamilani pa Mulungu, Mulungu wanu ndi Ambuye wa atate anu. Chifukwa anthu akusokera m’njira za chitaiko, osatha kuona Mulungu ndi maso awo, kapena kumva nyimbo Yake ndi makutu awo. Ndi momwe Tawapezera, monga nanunso muchitira umboni. Ndichifukwa chake miyambo yao yosanduka zophimba pakati pa iwo ndi mitima yao ndikuwachotsa iwo m’njira ya Mulungu, Wokwezeka, Wamkulu.

Muyenera kutsimikiza mwa inu nokha kuti ndithudi, iye amene samvera Wokongolayu wakananso kumvera Atumwi onse akale ndipo wasonyeza kunyada pamaso pa Mulungu kuyambira ku nthawi zosayamba mpaka ku nthawi zosatha.

Phunzirani bwino pemphero ili, O Ahmad. Lineneni m’masiku anu ndipo musadzilekelere nokha m’menemo. Pakuti ndithudi, Mulungu wamukonzera iye wakulinena mphoto ya ophedwa oyera mtima zana limodzi ndi kumtumikira m’maiko onse awiri. Zaulerezi Tazipereka kwa inu ngati mtulo ku mbali Yathu ndi chifundo chodzera ku malo Athu, kuti mukhale a iwo woyamika.

Pali Mulungu! Ngati wina ali m’zowawa kapena m’chisoni nawerenga Pempheroli ndi mtima wonse, Mulungu Adzakankha chisoni chake, nakonza zobvuta zake ndi kuchotsa zowawa zake. Ndithudi, Iye ndi Wachifundo, Wachisoni. Mayamiko akhale kwa Mulungu, Ambuye wa maiko onse.

#13478
- Bahá'u'lláh

 

PEMPHERO LA MOTO

Pemphero lowululidwa ndi Bahá’u’lláh lotchedwa “QadIhtaraqa ‘I-Mukhlisun”

Mdzina la Chauta, Mkhala kale, Wamkulukulu Ndithudi mitima ya okoma mtima yamezedwa ndi moto wampatuko: Lilikuti dangaliro lakuwala kwa maonekedwe Anu? O Okondedwa a mayiko?

Iwo okhala chifupi Nanu afulatiridwa Mu mdima wandiwe yani: Nanga kuli kuti kuwala kwa mbandakucha wa kugwirizananso ndi Inu? O Khumbo la mayiko. Matupi ya osankhidwa Anu ali chigonere wozizidwa pa mchenga wakutali Ili kuti nyanja ya kupezeka Kwanu, O Inu Odabwitsa wa mayiko?

Manja yofunafuna yakwezedwa kumwamba kwa Chisomo Chanu ndi kuwolowa manja. Ili kuti mvula yakupatsa Kwanu, O Woyankha a mayiko?

Osakhulupirira akwezeka nkhanza mbali zonse mmanja mwawo: Ili kuti mphamvu yakukaniza ya Cholembera Cha chilamulocho, O Ngwazi ya mayiko?

Kubwentha kwa agalu kwakula mbali zonse: Uli kuti mkango wamnkhalango ya ukulu Wanu, O Namkungwi wa mayiko? Chisanu chakutira anthu onse: Chili kuti chifundizi cha chikondi Chanu, O Moto wa mayiko?

Masautso afika pa msinkhu wake: Zili kuti zizindikiro za chitsogozo Chanu, O Chipulumutso cha mayiko? Mdima wakutira anthu ambiri: Kuli kuti kunyezimira kwa Ukulu Wanu, O Dangaliro la mayiko?

Makosi ya wanthu yasololokera ku umbanda: Nanga yali kuti malupanga yakulipsira Kwanu, O Wowononga wa mayiko? Kutsika kwafikapo pa mathero: Chili kuti chipilala cha chikumbutso cha Ulemelero Wanu, O Ulemerero wa mayiko?

Masautso amukuta Mvumbulutsi wa Dzina Lanu, wa Chifundo Chonse: Chili kuti chisangalalo cha kasupe wa tsiku la Chivumbulutso Chanu, O Chimwemwe cha mayiko? Mabvuto akulu awagwera anthu apadziko: Nanga chilikuti chizindikiro cha chimwemwe Chanu, O Chisangalaro cha mayiko?

Taonani malo a mbandakucha wa zizindikiro Zanu yamvekedwa ndi maganizo onyansa: Zili kuti zala za ukulu Wanu, O mphamvu za mayiko? Ludzu lagwira anthu anu onse: Uli kuti Mtsinje wa kuolawa manja Kwanu, O Chifundo cha mayiko?

Umbombo wagwira ukapolo anthu a padziko: Nanga kupatsa kwa umataya kuli kuti, O Ambuye wa mayiko? Taonani uyu wolakwiridwayo yekhayekha kuchilendo: Ali kuti ochereza akumwamba Kwa Chilamulo Chanu, O Wamkulu wa mayiko

Ndafulatiridwa ku dziko lachilendo: Chili kuti chizindikiro cha kukhulupirira Kwanu, O Wokhulupirira wa mayiko? Mpweteko wa imfa wayalidwa pa anthu onse: Nanga nyanja Yanu youluma yamoyo osatha ili kuti, O Moyo wa mayiko?

Kunong'ona kwa satana kwa nong'oneza cholengedwa chiri chonse: Nyenyezi zakugwa za moto wanu zili kuti, O Kuwala kwa mayiko? Uchidakwa wa udani wasintha mtundu wa anthu ambiri Ali kuti masiku a ungwiro, O Khumbo la mayiko?

Taonani Olakwiridwayo wamvekedwa ndi mazunzo pakati pa ma Siriya: Lili kuti Dangaliro la kuwala kwa mbandakucha Wanu, O Kuwala kwa mayiko? Taonani Ndaletsedwa kuyankhula: Tsono ndikuti kudzachokera kasupe wa nthetemya Zanu, O Mbalame ya mayiko?

Anthu ambiri akutidwa mu zikhulupiriro ndi maganizo osathandiza: Nanga zili kuti mboni za chitsimikizo Chanu, O Wotsimikiza wa mayiko? Bahá alinkutitimira m'nyanja ya msautso: Chili kuti Chombo cha chiombolo Chanu, O Mpulumutsi wa mayiko? Taonani Tsiku la Kasupe wa mawu Anu mu mdima wa chilengedwe: Dzuwa lamlengalenga wa chisomo Chanu lili kuti? O Woninkha Kuwala mayiko?

Nyali za chowonadi ndi chiyero, zakumvera ndi ulemu zazimitsidwa: Nanga zizindikiro za mkwiyo obwezera zili kuti, O Choyenda cha mayiko?Kodi simudamuoneko amene wapambana mwa Inu Mwini kapena amene asinkhasinkha pa zomwe zamugwera Iye mu njira ya Chikondi Chanu?

Tsopano cholembera changa chaima, O Wokondedwa wa mayiko. Nthambi za Uzimu za mtengo wa Lote, zakhadzuka kamba ka mphepo ya mkuntho ya chikonzero: Nanga zisalu zakutchinga Kwanu zili kuti, O Ngwazi ya mayiko?

Nkhopeyi yaphimbika mu dothi la mabodza: Uli kuti mweya wa chisoni Chanu, O Chifundo cha mayiko? Chovala chonyezima chadetsedwa ndi anthu a mabodza: Nanga chiyerocho chili kuti, O Okongoletsa mayiko?

Nyanja ya chisomo yadetsedwa ndi zomwe manja ya anthu yadzetsa: Ali kuti mafunde a mphatso Yanu, O Khumbo la mayiko? Khomo lotengera ku Malo a Uzimu lakhomedwa kudzera mmantha ya mazunzo Yanu: Uli kuti mpiringidzo wa kuwolowa manja Kwanu, O wotsegula wa mayiko?

Masamba yachita chikasu ndi mphepo zowononga ya poizoni: Ili kuti mitambo ya mvula yakuwolowa manja kwanu, O Wopatsa wa mayiko? Chilengedwe chadetsedwa ndi donthi la chifwirimbiti cha machimo: Uli kuti mweya wa kukhululukira Kwanu, O Wokhululukira wa mayiko?

Taonani mnyamatayu ali yekha m’chipululu: Ili kuti mvula ya chisomo cha kumwamba Kwanu, O Wopatsa wa mayiko? O Cholembela Chopatulika, Tamva kuitana konzuna mu dziko la ulemelero: Perekani khutu ku chimene Lilime lalikulu linena, O Wolakwiridwa wa mayiko!

Sichifukwa cha kuzizira, Kutentha kwa mawu anu kudakawululidwa, O Wofotokoza mwatchutchu wa mayiko? Sichifukwa cha mabvuto, Dzuwa la kudekha Kwanu lidakawala bwanji, O Wowala wa mayiko? Usalire chifukwa cha ochimwa. Iwe unalengedwa kuti ulimbe ndi kukumana nazo, O Wodekha wa mayiko?

Kuzuna kwake m’kotani kwa mzere wa mbandakucha wa Pangano pakati pa anthu osokoneza, ndi chofuna Chanu kwa Mulungu, O Wokonda wa mayiko. Chifukwa cha Inu chinsalu cha mtendere chaikidwa pa mwamba pa mapiri, ndipo nyanja ya chaulere ikuyendayenda, O Wong’anima wa mayiko?

Ndi kukhala Kwanu Dzuwa la Umodzi wanu lawala, ndi kuthamangitsidwa Kwanu dziko la Umodzi lapezeka. Khalani odekha, O Inu othamangitsidwa wa mayiko. Tapanga kutsitsidwa kukhala chobvala cha ulemelero, ndipo mabvuto chokongoletsera cha chihema Chanu, O Chonyaditsa cha mayiko.

Taonani mitima yadzala ndi udani, ndipo kusalabadira ndi Kwanu. O Inu wofufuta machimo wa mayiko. Pamene malupanga adza, pitani patsogolo! Pamene misikiro iwuluka, musaleke! O Inu wodzipereka wa mayiko?

Kodi simulira, kapena ndidzalire? Kapena ndilire chifukwa cha kuchepa kwa ngwazi Zanu. O Inu Amene mwapangitsa dziko kulira. Indetu, Ndamva kuitana Kwanu, O Wokondedwa wa Ulemerero Wonse; ndipo tsopano khope ya Bahá iwala ndi chifundizi cha mabvuto ndi moto wa kuwala kwa mawu Anu, ndipo Iye wayimirira mu chikhulupiliro pa malo a kudzipereka, kuyang’ana pa Khumbo Lanu. O Wopereka wa mayiko.

O 'Alí-Akbar, Pereka matamando kwa Ambuye wako chifukwa cha Pempheroli kuti upumeko kunukhira kwa mawu Anga, ndipo ziwani chimene chatisautsa Ife njira ya Mulungu, wokondeka wa mayiko onse. Ndipo ngati onse atumiki awerenga ndi kulingalira ichi, mudzayatsidwa mitsempha yawo moto umene udzayatsa lawi kudziko lonse.

#13479
- Bahá'u'lláh

 

PEMPHERO LA MTENDERE

O Inu Ambuye wokoma mtima! Inu mwalenga mtundu wonse wa anthu kuchokera kwa kholo limodzi. Inu mwalamulira kuti onse adzakhala abanja limodzi. Pamaso panu poyera iwo ali antchito Anu, ndipo mtundu wonse wa anthu wafungatiridwa pansi pa Chihema Chanu; onse asonkhana pamodzi ku Gome la Kuolowamanja Kwanu; onse awalitsidwa kupyolera mu kuwala kwa chisamaliro Chanu.

O Mulungu! Inu Ndinu wokoma mtima kwa onse, Inu mwapereka kwa onse zosowa zawo, mumafungatira onse, mumapatsa moyo kwa onse. Inu mwawapatsa yense waiwo ndi iwo onse luso la nzeru, ndipo onse amizidwa mu Nyanja ya Chifundo Chanu.

O Inu Ambuye wokoma mtima! Gwirizanitsani onse. Pangani kuti zipembedzo zigwirizane ndipo pangani kuti mitundu yonse ikhale mtundu umodzi, kuti aonane wina ndi mzake ngati abanja limodzi ndipo dziko lonse lapansi ngati kukhomo kwawo kumodzi. Azikhalira pamodzi mu kumvana kwangwiro.

O Mulungu! Kwezani m’mwamba kwambiri mbendera ya umodzi wa mtundu wa anthu. O Mulungu! Khazikitsani Mtendere Waukulu Koposa. Umbani Inu, O Mulungu, mitima yonse pamodzi. O Inu Atate wokoma mtima, Mulungu! Sangalatsani mitima yathu kupyolera mu pfungo labwino la chikondi Chanu.

Walitsani maso athu kupyolera mu kuwala kwa Chitsogozo Chanu. Sangalatsani makutu athu ndi kukoma kwa Liu Lanu, ndipo tifungatireni mu Tchinga la Chisamaliro Chanu. Inu Ndinu Wanyonga ndi Wamphamvu, Inu ndi Wokhululukira ndipo Ndinu Nokha Amene simulabadira zoperewera za mtundu wonse wa anthu.

#13480
- `Abdu'l-Bahá

 

PEMPHERO LOCHEZERANA

(Mapemphero ili limawerengedwa pa Manda a Bahá’u’lláh ndi Báb. Limagwiritsidwanso ntchito pokumbukira kubadwa kwa Bahá’u’lláh ndi Báb komanso kukumbukira kuwera kumwamba kwa Bahá’u’lláh ndi kuphedwa kwa Báb)

Mayamiko amene m’bandakucha wake waonekera ndi nkhope Yanu yolemekezeka kopambana, ndi ulemelero umene wawala kuchokera kwa Wokongola mowala kopambana, akhale pa Inu, O Inu Amene Muli Maonekedwe a Ulemelero, ndi Mfumu Yamuyaya, ndi Ambuye wa onse amene ali m’mwamba ndi padziko lapansi!

Ine nditsimikiza kuti kupyolera mwa Inu Ufumu wa Mulungu ndi Ukulu wa Mulungu ndi Ulemelero Wake, zinabvumbulutsidwa, ndipo nthanda za kunyezimira Kwake kwakale-kale zagwetsa kuwala kwao kumwamba kwa lamulo Lanu losasinthika, ndipo kukongola kwa Wosaonekayo kwawala pamwamba pa zolengedwa zonse.

Nditsimikizanso kuti ndi kuyenda kwa Cholembera Chanu Chokha, Chifuniro Chanu chakuti: “Khala Iwe” chakwaniritsidwa, ndiponso chinsinsi cha Mulungu chaululidwa, ndipo zinthu zonse zolengedwa zaitanidwa kumoyo ndi Zibvumbulutso zonse zatsika pansi.

Ine ndichitira umboninso, kuti kupyolera mwa kukongola Kwanu, Kukongola kwa Wopembedzayo kwaonetsedwa, ndipo kupyolera mwa Nkhope Yanu, Nkhope ya Wofunikayo Yawala, ndi kuti kupyolera mwa mau Anu, Inu mwaganizira bwino pakati pa zolengedwa zonse, kuwapangitsa amene ali wopembedza Inu kukwera ku nsonga ya ulemelero, ndi wosakhulupilira kugwera m’mbuna yakuya.

Ine ndichitira umboni kuti iye amene wakudziwani Inu wadziwa Mulungu, ndi iye amene wafika pamaso Panu wafika pamaso pa Mulungu. Chomwecho nkwakukulu kudalitsidwa kwa iye amene wakhulupilira mwa Inu, ndi mwa zizindikiro Zanu, ndipo walemekezedwa ndi kukomana Nanu, ndipo wafika pa zokoma za chifuniro Chanu, ndi kukuzungulirani ndi kuima patsogolo pa Mpando Wanu.

Tsoka kwa iye amene wakulakwirani Inu, ndipo wakukanani Inu, ndipo sanabvomera zizindikiro Zanu, ndipo watsutsa ufumu Wanu, ndipo wakuukirani Inu, ndipo wasonyeza kunyada pamaso Panu, ndipo wakangana ndi maumboni Anu, ndipo wathawa chilamulo Chanu ndi ulamuliro Wanu ndi kuwerengedwa limodzi ndi wosakhulupilira amene maina awo asindikizidwa ndi zala za kulamula Kwanu pamauthenga Anu oyera.

Chomwecho, uzirani kwa ine, O Mulungu wanga ndi Wokondedwa wanga, kuchokera kudzanja lamanja la chifundo Chanu ndi chisoni cha kukonda Kwanu, mphweya woyera wa ubwino Wanu, kuti zindichotse ine ndekha ndi m’dziko lapansi ndi kunditengera ku mabwalo a kuyandikira kwanu ndi pamaso Panu. Muli ndi mphamvu kuchita zomwe zakukomerani. Inu ndithudi Mwakhala Wamphamvu koposa zonse.

Chikumbukiro cha Mulungu ndi mayamiko Ache, ndi Ulemelero wa Mulungu ndi kuwala kwake zikhale pa Inu, O Inu Amene Muli kukongola Kwake! Ndichitira umboni kuti diso la chilengedwe silinaone wina wolakwiridwa monga Inu. Munamizidwa masiku onse amoyo Wanu pansi pa nyanja ya zowawa. Pa nthawi yina Munali m’maunyolo ndi nsinga; pa nthawi yinanso Munaopsezedwa ndi lupanga la adani Anu. Komabe, ngakhale ziri chomwecho munalamulira wanthu onse kutsata zonse zimene Munalangizidwa ndi Iye Amene Ali Wodziwa Zonse, Wanzeru Zonse.

Lolani mzimu wanga ukhale nsembe chifukwa cha zolakwa zimene Inu Munabvutika nazo ndi moyo wanga ukhale chopereka chifukwa cha mikwingwirima yomwe Munapwetekedwa nayo. Ndipempha Mulungu,mwa Inu ndi mwa iwo amene nkhope zawo zawalitsidwa ndi kuunika kwa Nkhope Yanu, ndi iwo amene, chifukwa cha chikondi Chanu, atsata zonse zimene anafunsidwa, kuchotsa zophimba zomwe zabwera pakati pa Inu ndi zolengedwa Zanu, ndi kundipatsa ine zabwino padziko lino ndi dziko lirinkudza. Inu zoonadi Ndinu

Wamphamvu Zonse, Wam’mwamba-mwamba, Woyerayera, Wokhululukira Nthawi Zonse, Wachifundo Chozama.

Dalitsani, O Ambuye Ambuye wanga, Mtengo Wopatulika wa Lote ndi masamba ake, ndi makungwa ake ndi nthambi zake, ndi misinde yake ndi mphukira zake malingana ndi momwe maina Anu opambana adzakhalira ndi maudindo Anu wotchuka kwambiri adzatha. Uchinjilizeni chomwecho kuchokera ku zokhumudwitsa za achiwembu ndi magulu ankhanza.

Inu Ndinu, zoonadi Wamphamvu Zonse, Wolimba Kwambiri. Dalitsaninso, O Ambuye Mulungu wanga, antchito Anu ndi adzakazi Anu amene afika kwa Inu. Inu zoonadi Ndinu Wachifundo Chonse, amene chisomo Chake m’chamuyaya. Palibe Mulungu wina koma Inu, Wokhululukira-nthawi Zonse, Wokomamtima.

#13481
- `Abdu'l-Bahá