Return to BahaiPrayers.net
Facebook
Iye ndi Mulungu, ndi Iye Wokwezeka, Ambuye wokoma mtima ndi wa chaulere! Ulemelero ukhale kwa Inu, O Inu Mulungu wanga, Ambuye Mwini-mphamvu.
Ine ndichitira umboni ku Umwini-mphamvu Wanu, Ukulu Wanu, Ufumu Wanu, Kukomamtima Kwanu, Chisomo Chanu ndi Mphamvu Yanu, Umulungu Wanu, umodzi wa khalidwe Lanu, kupatulika Kwanu ndi kukwezeka Kwanu pamwamba padziko la chilengedwe ndi zonse ziri m’menemo.
O Mulungu wanga, Mukundiona ine ndadzipatula kuzinthu zonse koma kwa Inu, ndakakamira kwa Inu ndi kutembenukira kunyanja ya mphatso Zanu, kumwamba kwa chaulere Chanu, ku Nthanda ya Chisomo Chanu.
Ambuye! Ine ndichitira umboni kuti mwa wantchito Wanuyu munaikamo cholowa Chanu, ndiwo mzimu umene Inu Munapatsa nawo moyo kudziko lapansi.
Ndikupemphani kupyolera kwa Chibvumbulutso Chanu, mwa chifundo Chanu. Bvomerani zimene iye wazichita bwino m’masiku Anu. Mloleni chomwecho kuti abvekedwe ndi ulemelero wa ubwino Wanu ndi kuwalitsidwa ndi kulandilidwa Kwanu.
O Ambuye wanga, ineyo ndi zolengedwa zonse tichitira umboni kumphamvu Zanu ndi kukupemphani kuti musausiye mzimu uwu kutali ndi Inu umene wakwera kwa Inu, kumalo Anu akumwamba, ku Paradiso Wanu wokwezeka ndikumpumulo wofupikira kwa Inu.
O Inu amene Muli Ambuye wa anthu onse! Lolani tsono, O Mulungu wanga, kuti wantchito Wanuyu achezerane ndi osankhika Anu, Oyera Anu ndi Atumiki Anu m’malo a kumwamba amene cholembera sichingathe kunena kapena lilime kusimba.
O Ambuye wanga, wosaukayo wathamangiradi ku Ufumu wa chuma Chanu, mlendoyu wafika kwao mkati mwa mabwalo Anu, iye waludzu ku mtsinje wakumwamba wa chaulere Chanu. Musam’mane, O Ambuye gawo lake la phwando la chisomo Chanu ndi Chifundo cha chaulere Chanu. Inu zoonadi Ndinu Wamphamvu-zonse, Wachisomo, Wachaulere!
O Mulungu wanga cholowa Chanu chabwezedwa kwa Inu. Nkoyenera chisomo Chanu ndi chaulere Chanu zimene zazungulira ulamuliro Wanu mdziko lapansi ndi kumwamba, kupereka kwa yemwe Mwamlandira tsopanoyu mphatso Zanu ndi madalitso Anu, ndi zipatso za mtengo wa chisomo Chanu! Muli ndi mphamvu kuchita monga momwe Mufunira. Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wachisomo, Wachaulere chodzaza, Wachisoni, Wopatsa, Wokhululukira,
Wamtengowapatali, Wodziwa-zonse.
Ndichitira umboni, O Ambuye wanga, kuti Inu Mwawafunsa anthu kulemekeza mlendo wao, ndipo yemwe wakwera kwa Inu wafikadi kwa Inu ndipo walandiridwa pamaso Panu. Chitanayeni chomwecho malinga ndi chisomo Chanu ndi chaulere Chanu! Mwaulemerelo Wanu, Ine ndidziwa kwa mtheradi kuti simudzakana chimene Inu mwawalamulira akapolo Anu kapena simudzam’mana iye amene wakakamira pa chingwe cha chaulere Chanu ndi kukwera ku kasupe wa chuma Chanu.
Kulibe Mulungu wina koma Inu, M,modzi Yekha, Wamphamvu, Waponse-ponse, Wachaulere.
- Bahá'u'lláh