ANA (#13449)

O Ambuye wanga! Pangani kukongola Kwanu kukhale chakudya changa, ndikupezeka Kwanu ndi chakumwa changa ndipo chitamando Chanu ndiye kuchita kwanga ndipo kukumbukira Inu ndiye mzanga, ndipo mphamvu ya Ulumuliro Wanu ndi chithandizo changa, malo Amene Mukhala ndi ku khomo kwanga, ndipo malo anga omwe ndikhala ndi malo omwe inu mwawadalitsa kuchokera ku muyeso umene mwaupereka kwa iwo amene azitsekera poziphimba kwa inu. Inu ndinu, ndithudi, wamkulu, wa ulemelero onse, wamphamvu zonse.”

-Bahá'u'lláh
-----------------------

ANA (#13450)

O Inu a Chifundo Ambuye! Ndine mwana wamng’ono, ndikwezeni ine pondilora ine ku ufumu. Ndili wa dziko lapansi, ndipangeni ndikhale wakumwamba, ine ndili wotsika padziko, ndiloleni ine ndikhale wa maiko am’mwamba; mdima, ndifuteni ine kuti ndikhale woyera; chinthu cha dziko ndipangeni ine wauzimu, ndipo ndipatseni kuti ndi bvumbulutse mphatso Zanu 	zopanda 	malire. 	Inu 	ndinu 	Wamphamvu, Wachikondi Chonse.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

ANA (#13446)

O Mulungu wanga, Okondedwa wanga, khumbo la mtima wanga.

-The Báb
-----------------------

ANA (#13447)

O Mulungu! Lelani kakhanda aka pa chifungatiro chachikondi Chanu, ndipo mukapatse mkaka wochokera kumaere a Mphatso Yanu. Samalirani kachomeraka m’munda wamaluwa wa chikondi Chanu ndikukathandiza kukula kubzolera mumbvumbi wa chaulere Chanu. Kapangeni kukhala kamwana ka Ufumu ndipo katsogozeni kumwamba Kwanu. Inu Ndinu wamphamvu ndi wokoma mtima, ndipo Inu Ndinu Wopatsa, Wosamana, Ambuye a chaulere chopambana.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

ANA (#13448)

O Mulungu! Phunzitsani ana awa. Ana awa ali zomera za m’munda Wanu wazipatso, maluwa a M’dimba Lanu, Lozesi wa m’munda Wanu. Lolani kuti mvula Yanu iwagwere; lolani kuti dzuwa la choonadi liwalire pa iwo ndi chikondi Chanu. Lolani kuti mweya Wanu uwatsitsimutse mwakuti iwo aphunzitsidwe, akule ndipo adzadziwe, ndi kuoneka okongola kweni-kweni. Inu Ndinu Wopatsa. Inu Ndinu Wachisoni.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

ANA (#13451)

O Ambuye anga! O Ambuye anga! Ine ndine mwana wa zaka zochepa. Ndidyetseni ine kuchokera ku mawere a chifundo Chanu, ndipangeni ine kukhala muchifungatiro chachikondi Chanu, ndiphunzitseni ine musukulu ya chitsogozo Chanu ndipo mundipambanitse ine pansi pa nthunzi wa mphatso Yanu. Ndilanditseni ine kuchokera mu mdima, ndipangeni ine kukhala kuwala konyezimira; ndichotsereni ine kusakondwa, ndipangeni ine kukhala duwa m’munda wa lozesi, ndiwalitseni ine kukhala wantchito pakhomo Lanu loyera ndipo perekani kwa ine makhalidwe a umunthu ndi chilengedwe cha chiyero; ndipangeni ine chiyambi cha mphatso kwa wanthu adziko lapansi ndipo vekani mutu wanga ndi chisoti cha moyo wosatha. Indetu, Inu ndinu Wamphamvu, Wamkulu, Woona, Wakumva.”

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

