KUPHUNZITSA (#13467)

O Mulungu! O Mulungu! Ino ndi mbalame yothyoka phiko ndipo kuwuluka kwake ndi kwapang’onopang’ono, ithandizeni kuti ithe kuwuluka kufika kunsonga ya chuma ndi chipulumutso, iwuluke ulendo wake ndi chimwemwe ndi chisangalaro chonse kunka mu mlengalenga mopanda malire, kwezani nyimbo yake m’Dzina Lanu Lalikulu mu zigawo zonse, sangalatsani makutu ndi kuyitanaku, ndikuwalitsa maso pakuwona zizindikiro za chitsogozo!  
O Ambuye! Ndine m’modzi, ndekha, ndi wopepuka. Kwa ine kulibe mtsamiro wina uliwonse koma Inu Nokha, ndilibe mthandizi Ndinu Nokha ndipo ndilibe mtonthozi wina woposa Inu. Ndilimbikitseni mu ntchito Yanu, ndithandizeni kulankhula za nzeru Zanu pakati pa zolengedwa Zanu. Indetu, Inu Ndinu mthandizi wa ofooka ndi mtchinjirizi wa ang’onoang’ono, ndipo indetu, Inu Ndinu Wamphamvu, Wamkulu ndi Wosakakamizidwa!

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

KUPHUNZITSA (#13468)

O Inu Mulungu Wosafaniziridwa! O Inu Ambuye wa Ufumu! Miyoyo iyi ndi ankhondo Anu akumwamba. Athandizeni iwo, ndipo ndi magulu Akhamu Lapamwamba Muwapambanitse; kuti yense wa iwo akhale ngati gulu la nkhondo ndi kugonjetsa maikowa kupyolera mu chikondi cha Mulungu ndi kuwala kwa uzimu kwa Chiphunzitso Chanu.  
O Mulungu! Mukhale wowatchinjiriza ndi Mthandizi wao, ndipo m’chipululu, m’phiri, m’chigwa, m’nkhalango, m’madambo ndi m’nyanja, khalani Inu wowasangalatsa – kuti alire kupyolera mu mphamvu ya Ufumu ndi kuuzira kwa Mzimu Woyera!  
Indetu, Inu Ndinu Wamphamvu, Wamkulu ndi Mwinimphamvu, ndiponso Inu Ndinu Wanzeru, Wakumva ndi Woona.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

KUPHUNZITSA (#13469)

O Mulungu wanga! O Mulungu wanga! Inu mukundiona ine mukutsika kwanga ndi kufooka kwanga, otanganidwa ndi ntchito yaikulu, ndikutsimikiza kukweza liwu Lanu pakati pa magulu a wanthu ndi kufalitsa ziphunzitso Zanu pakati pa anthu Anu. Ndingapambane bwanji popanda kuthandizidwa ndi Inu ndi kuuzira kwa Mzimu Woyera, ndithandizeni kuti ndipambane ndi makamu a ufumu Wanu wa ulumerero. Ndikundipatsa chitsimikizo Chanu chimene pachokha chikhoza kusintha kachilombo kakang’ono kwambiri koluma kukhala chiombankhanga, kadontho ka madzi kukhala mitsinje ndi nyanja ndipo kanthu kakang’ono kukhala kuwala ndi dzuwa?  
Inu ndinu Wamphamvu ndi Wochita chilichonse chimene mufuna.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

