MADZULO (#13443)

O Mulungu wanga, Mbuye wanga, mathero Achofuna changa, uyu, wantchito Wanu, afuna kugona mum’thunzi wa chifundo Chanu, ndikupumula pansi pa chifungatira cha chisomo Chanu, akupempha chisamaliro Chanu ndi chitetezo Chanu.  
Ine ndikupemphani Inu, O Ambuye wanga, kuti ndi diso Lanu limene siligona, mulonde maso anga kuti asayang’ane china pambali pa Inu. Limbikitsani, choncho masomphenya ake kuti aone zizindikiro Zanu, ndikuyang’ana ku mzere wa Chibvumbulutso Chanu. Inu ndinu amene patsogolo pa zibvumbulutso za ukulu Wanu, maonekedwe amphamvu agwedezeka.  
Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wamphamvu Zonse, Wogonjetsa Onse, Wosakakamizidwa.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

MADZULO (#13444)

*O ofufuza Choonadi! Ngati ukukhumba kuti Mulungu atsegule maso ako, uyenera kupempha kwa Mulungu, kupemphera ndi kuyankhula Naye pakati pausiku, ndi kunena:  
 O Ambuye, Ndatembenuzira nkhope yanga ku ufumu 
Wanu wa umodzi ndi kudzimiza m’nyanja ya chifundo Chanu. O Ambuye, walitsani maso anga powona kuwala Kwanu pakati pa usiku uno, ndi kundipanga kukhala osangalala ndi vinyo wa chikondi Chanu mu m’badwo wopambanawu. O Ambuye, ndipangeni kuti ndimve kuitana Kwanu, ndipo tsengulani pamaso anga zitseko zakumwamba Kwanu, choncho kuti ndiwone kuwala kwa ulemerero Wanu ndi kukopedwa ndi kukongola Kwanu.  
Indetu, Inu ndi Wopatsa, Woolowamanja, Wachifundo, Wokhululukira.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

