M’BANDAKUCHA (#13441)

O Mulungu wanga ndi Mbuye wanga! Ine ndine wantchito Wanu, ndi mwana wantchito Wanu. Ndadzuka pamphasa panga m’bandakucha uno pamene nthanda ya umodzi wanu yaunikira kuchokera m’bandakucha wa chifuniro Chanu, ndipo kuunika kwake kwakwanira padziko lonse lapansi, monga momwe kunalonjezedwera mu Mabuku a Chilamulo Chanu.  
Matamando akhale kwa Inu. O Mulungu Wanga, Kuti tadzuka kuulemelero ndi kuona kuwala kwa Nzeru Zanu. Tumizani pansi pano, tsono, kwa ife, O Ambuye wanga, chomwe chidzatipanga ife kusiya aliyense koma Inu, chomwe chidzatichotsera kumangika ndi kalikonse, koma Inu Nokha. Ndilembereninso ine, pamodzi ndi iwo amene ali okondedwa anga, ndi abale anga, amuna ndi akazi omwe, zabwino zadziko lino ndi za dziko liri mkudza. Tisamalireni, tsono, kubzolera mu chitetezo Chanu chosalephera, O Inu Wokondedwa wa chilengedwe chonse ndi khumbo la miyamba yonse, kuchokera kwa iwo amene munawapanga kukhala cholowa cha iye wonong’ona zoipa, amene anong’ona m’mitima ya anthu. Muli ndi mphamvu kuchita monga momwe mufunira. Indetu, Ndinu Wamphamvu zonse, Wothandiza pa tsoka, Wodzidalira Nokha.  
 
Dalitsaninso, O Ambuye Mulungu wanga, Iye amene Inu munamuika pamwamba pa maudindo Anu akulu, amene kubzolera mwa Iye, Inu mwasiyanitsa pakati pa anthu a umulungu ndi oipa, ndipo mwachisomo tithandizeni kuchita zomwe Inu muzikonda ndi kuzifuna. Adalitseni Inu, koposetsa, O Mulungu wanga, iwo amene ali Mau  anu ndi Malemba Anu, ndi iwo amene aika nkhope zao kwa Inu, ndikutembenukira ku nkhope Yanu, ndikumvera kuitana kwanu. Inu, ndithudi, Ndinu Mbuye ndi Mfumu ya anthu onse, ndipo muli wamphamvu pa zinthu zonse.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

