OMWALIRA (#13474)

Ulemelero ukhale kwa Inu, O Ambuye Mulungu wanga! Musanyasidwe naye iye amene Inu mwamkweza kupyolera mu mphamvu ya ufumu Wanu wamuyaya, ndi kumsiya kutali ndi Inu, amene Inu Munamlola kulowa m’chihema Chanu cha kunthawi zosatha. Kodi Mungamtaye, O Mulungu wanga iye amene Inu Mwamphimba ndi Ufumu Wanu ndipo mungamtembenukire, O chifuniro changa amene Mwakhala pothawira pake? Mungamunyoze iye amene Inu Mwamtukula, kapena Kumuiwala iye amene Inu munanthandiza kukukumbukirani? Wolemekezedwa, kwamtheradi Muli Wolemekezedwa Inu! Inu muli Amene kuyambira pachiyambi Mwakhala Mfumu ya chilengedwe chonse ndi Woyendetsa Wake ndipo mpaka ku nthawi zosatha Mudzakhalabe Ambuye wa zolengedwa zonse ndi Mkozi Wake.  
Wolemekezedwa muli Inu, O Mulungu wanga! Ngati Muleka kuchitira chisoni antchito Anu, ndani nanga angawachitire chisoni? Ndipo ngati Mukana kudyetsa okondedwa Anu, kuli ndaninso woti angawadyetse? Wolemekezedwa, kwamtheradi Muli Wolemekezedwa 
Inu! Inu Mulambiridwa m’choonadi Chanu, ndipo Inu ndithudi ife tonse tikupembedzani, ndipo Inu Muli woonekera m’chilungamo Chanu, ndipo kwa Inu tonse, ndithu tichitira umboni. Inu muli, mchoonadi, wokondedwa mchisomo Chanu. Palibe Mulungu wina koma Inu Wothandiza pa Tsoka, Wosasowa kanthu.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

OMWALIRA (#13475)

Iye ndi Mulungu, ndi Iye Wokwezeka, Ambuye wokoma mtima ndi wa chaulere! Ulemelero ukhale kwa Inu, O Inu Mulungu wanga, Ambuye Mwini-mphamvu. 
Ine ndichitira umboni ku Umwini-mphamvu Wanu, Ukulu Wanu, Ufumu Wanu, Kukomamtima Kwanu, Chisomo Chanu ndi Mphamvu Yanu, Umulungu Wanu, umodzi wa khalidwe Lanu, kupatulika Kwanu ndi kukwezeka Kwanu pamwamba padziko la chilengedwe ndi zonse ziri m’menemo.  
O Mulungu wanga, Mukundiona ine ndadzipatula kuzinthu zonse koma kwa Inu, ndakakamira kwa Inu ndi kutembenukira kunyanja ya mphatso Zanu, kumwamba kwa chaulere Chanu, ku Nthanda ya Chisomo Chanu.  
Ambuye! Ine ndichitira umboni kuti mwa wantchito Wanuyu munaikamo cholowa Chanu, ndiwo mzimu umene Inu Munapatsa nawo moyo kudziko lapansi.  
Ndikupemphani kupyolera kwa Chibvumbulutso Chanu, mwa chifundo Chanu. Bvomerani zimene iye wazichita bwino m’masiku Anu. Mloleni chomwecho kuti abvekedwe ndi ulemelero wa ubwino Wanu ndi kuwalitsidwa ndi kulandilidwa Kwanu.  
O Ambuye wanga, ineyo ndi zolengedwa zonse tichitira umboni kumphamvu Zanu ndi kukupemphani kuti musausiye mzimu uwu kutali ndi Inu umene wakwera kwa Inu, kumalo Anu akumwamba, ku Paradiso Wanu wokwezeka ndikumpumulo wofupikira kwa Inu.  
O Inu amene Muli Ambuye wa anthu onse! Lolani tsono, O Mulungu wanga, kuti wantchito Wanuyu achezerane ndi osankhika Anu, Oyera Anu ndi Atumiki Anu m’malo a kumwamba amene cholembera sichingathe kunena kapena lilime kusimba.  
O Ambuye wanga, wosaukayo wathamangiradi ku Ufumu wa chuma Chanu, mlendoyu wafika kwao mkati mwa mabwalo Anu, iye waludzu ku mtsinje wakumwamba wa chaulere Chanu. Musam’mane, O Ambuye gawo lake la phwando la chisomo Chanu ndi Chifundo cha chaulere Chanu. Inu zoonadi Ndinu Wamphamvu-zonse, Wachisomo, Wachaulere!  
O Mulungu wanga cholowa Chanu chabwezedwa kwa Inu. Nkoyenera chisomo Chanu ndi chaulere Chanu zimene zazungulira ulamuliro Wanu mdziko lapansi ndi kumwamba, kupereka kwa yemwe Mwamlandira tsopanoyu mphatso Zanu ndi madalitso Anu, ndi zipatso za mtengo wa chisomo Chanu! Muli ndi mphamvu kuchita monga momwe Mufunira. Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wachisomo, Wachaulere chodzaza, Wachisoni, Wopatsa, Wokhululukira, 
Wamtengowapatali, Wodziwa-zonse.  
Ndichitira umboni, O Ambuye wanga, kuti Inu Mwawafunsa anthu kulemekeza mlendo wao, ndipo yemwe wakwera kwa Inu wafikadi kwa Inu ndipo walandiridwa pamaso Panu. Chitanayeni chomwecho  malinga ndi chisomo Chanu ndi chaulere Chanu! Mwaulemerelo Wanu, Ine ndidziwa kwa mtheradi kuti simudzakana chimene Inu mwawalamulira akapolo Anu kapena simudzam’mana iye amene wakakamira pa chingwe cha chaulere Chanu ndi kukwera ku kasupe wa chuma Chanu.  
Kulibe Mulungu wina koma Inu, M,modzi Yekha, Wamphamvu, Waponse-ponse, Wachaulere.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

OMWALIRA (#13476)

*(Pempheroli liyenera kugwiritsidwa kwa a Bahá’í okha amene ali ndi zaka zoyambila  “Ndi pemphero lokhali lokakamiza la chiBahá’í limene limanenedwa pa gulu; liyenera kunenedwa ndi modzi mwa okhulupilira pamene onse abwerapo atayima…” –Kitáb-I-Aqdas)  
 O Mulungu wanga! Uyu ndi mtumiki Wanu ndi mwana wa mtumiki Wanu amene anakhulupirira Inu ndi zizindikiro Zanu, ndi kutembenukira nkhope yake kwa Inu, ndi kudzipatula kotheratu ku zonse koma Inu Nokha.  
Inu zowonadi Ndinu mwa amene awonetsa chifundo wa chifundo chonse. Chitanayeni, O Inu Amene Mukhululukira machimo a anthu ndi kukwirira zoyipa zawo, monga momwe kufunikira m’mwamba mwa chaulere Chanu ndi nyanja ya chisomo Chanu. Mulowetseni kumalo a chifundo Chanu chachikulu amene analipo asanakhale maziko apansi ndi kumwamba. Kulibe Mulungu wina koma Inu Nokha, Wokhululukira Nthawi Zonse, wa Chaulere Chonse.  
Onena pempheroli anene:  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tipembedza Mulungu (19)  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tigwada pamaso pa Mulungu (19)  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tili wodzipereka kwa Mulungu (19)  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tiyamika Mulungu (19)  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tithokoza Mulungu (19)  
“Alláh-u-Abhá” (kamodzi)  
Ife tonse, indetu, tili ndi chipiriro mwa Mulungu (19) 
 Bahá’u’lláh  
*(Ngati womwalira ali mkazi, wonena pemphero anene: Uyu ndi mdzakazi Wanu ndi mwana wa mdzakazi Wanu………)  
 
 O Mulungu wanga! O Inu wokhululukira machimo, Wopereka mphatso, Wochotsa masautso! Indetu, ndikupemphani kukhululukira machimo a iwo amene asiya mayala a thupi ndi kukwera kudziko lauzimu.  
O Mbuye wanga! Ayeretseni ku zoipa, achotsereni chisoni, ndipo sandulizani mdima wawo ukhale kuwala. Apangeni kulowa mmunda wa chimwemwe, atsukeni ndi madzi woyerayera, ndipo aloleni kuti awone kuwala Kwanu paphiri lalitali koposa.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

