ULENDO (#13484)

Ndadzuka m’mawa uno ndi chisomo Chanu, O Mulungu wanga, ndikunyamuka pakhomo panga ndi kukhulupirira kotheratu mwa Inu, ndi kudzipereka ndekha ku chisamaliro Chanu. Tumizani tsono, pa ine, kuchokera ku mwamba kwa chifundo Chanu, madalitso ochokera kwa Inu, ndipo Mundilole ndibwerere kwathu bwino monga momwe Munandilolera kunyamuka muchitetezo Chanu, ndi maganizo anga onse ali pa Inu. Kulibe Mulungu wina koma Inu Nokha, M’modzi Yekha, Wosafanizilika, Wodziwa Zonse, Wanzeru Zonse.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

ULENDO (#13485)

O Mulungu, Mulungu wanga! Ndanyamuka pa khomo langa, kugwiritsitsa chingwe cha chikondi Chanu, ndipo ndadzipereka ndekha kwathuthu ku chisamaliro Chanu ndi chitetezo Chanu. Ndikupemphani Inu ndi mphamvu Yanu imene Inu mwateteza nayo okondedwa Anu ku zopinga ndi makhalidwe oipa, ndi kwa ankhanza ndi achiwembu amene akhala kutali ndi Inu, nditetezeni ine ndi mphatso Zanu ndi chisomo Chanu. Ndiloleni, tsono, ndibwerere kwathu ndi mphamvu Zanu ndi nyonga Zanu.  
Inu, Choonadi, Wamphamvu Zonse, Wothandiza pa Tsoka, Wodzidalira Nokha.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

