Return   Facebook

The Universal House of Justice

Ridván 2023

To the Bahá’ís of the World

Dearly loved Friends,

Tili ndi chimwemwe chachikulu poyankhula ku mbumba yomwe malingaliro ake apamwamba akugwirizana ndi kuyitanidwa kwake kwakukulu. Ndichikondi chachikulu bwanji, inde chachikulu zedi chikondi chathu pa inu, momwe mizimu yathu inthunthumira ndi m’mene tikuona kuyesetsa kwanu kodzipereka ndi kowona mtima, kukhala miyoyo youmbidwa ndi Ziphunzitso za Bahá’u’lláh ndi kupereka madzi opatsa moyo a Chibvumbulutso Chake kudziko la ludzu. Nzeru ya cholinga chanu chachikulu ndiyowonekeratu. Kuphunzitsa ndi kuzamitsa, ntchito za chitukuko, ndikutenga nawo mbali muzokambirana zam’madera zikupita chitsogolo, ndipo limodzi zinthu izi zikuwonekeratu munkwamba. Nkutinso kwina izi zikuwonekera kupambana komwe chiwerengero chachikulu chikuchita ntchito zosiyana-siyana, iri yonse mwa iyo ndi chida chotsanulira mphamvu za Chipembedzo zomanga dera.

Miyezi khumi ndi iwiri yadutsapo chiyambireni Pulani iyi ya zaka Zisanu ndi zinayi, tiri okondwa kuona momwe ntchito yauzimu ya dziko lonse yasunthira ndi kupereka mangolomera kwa abwenzi ndikupereka mphamvu ku mbali zina za ntchito. Mosazengereza, chidwi chinalunjikitsidwa kuika mapulani amene awonetsetse kuti m’dziko ndi m’chigawo chilichonse mutuluke mkwamba umodzi umene wadutsa mtunda wachitatu: malo amene chiwerengero chachikulu cha anthu akugwira ntchito limodzi ndi kusonkhera ku umoyo wa mbumba wotaka-taka. Pozindikira, komabe, kuti golo la zaka makumi awiri ndi zisanuzi ndikukhadzikitsa ndondomeko yakathithi yakukula mu mkwamba uli onse padziko lapansi, okhulupilira ndi okonzekanso kutsegula mikwamba yatsopano ku Chipembedzo komanso kuwonjezera kuyesetsa kwawo m’malo momwe muli kale ndondomeko ya kukula mwa kathithi. Pali kuzindikira kwakukulu zamwayi wakuti akashole (mapayoniya) adzuke mbali zonse za dziko lapansi—khwimbi lamizimu yodzipereka ikulingalira momwe ingadzukire kuchitapo kanthu pa mwayi umenewu, ndipo mizimu ina yambiri yapita kale ku ukashole, mowonekeratu kumadera a kwawo komweko komanso mochuluka kumaiko ena. Iyi ndi imodzi mwanjira zimene, momwe tidaganizira, zikuonetsa mzimu wa kuthandizana omwe ukuonetsedwa ndi abwenzi konse-konse. Mbumba zomwe mphamvu zamangidwa zadzipereka kuthandiza kupita chitsogolo komwe kukuchitika malo osiyana— mum’kwamba, m’chigawo, m’dziko angakhalenso mukontinenti—ndipo njira zaluso zapezeka zoperekera chilimbikitso kuchokera m’tali-m’tali ndikulora kuphunzira kuti kufale mwachindunji. Panopa, njira zosonkhanitsira pamodzi zophunziridwa mu mkwamba, kuti zithandizire kupanga mapulani kudera ndi kwina kulikonse, zikugwiritsidwa ntchito. Takhala okhutitsidwa kuona kuti chidwi chapadera chikuyikidwa pa kuphunzira zamomwe machitidwe apamwamba pa nkhani ya maphunziro a insitichuti kungapitire patsogolo. Pomwe maphunziro a insitichuti akhazikika m’dera zotsatira zake ndi zowonekeratu. Mwachitsanzo, umboni ndi kumalo kumene kukuchitika zochita-chita zakathithi komwe anthu ake atenga maphunziro a insitichuti kuti ndi chida chawo champhamvu: chida chimene chitukuko chake achitenga kukhala udindo wawo waukulu. Pozindikira kuti makomo a Chipembedzo amakhala otsegula nthawi zonse, okhulupilira akuphunzira momwe angaperekere chirimbikitso kwa iwo amene ali okonzeka kulowa. Kuyenda ndi mizimu yotereyi, ndikuyithandiza kuwoloka malire, ndimwayi komanso chisangalaro chapadera; muchikhalidwe chiri-chonse, pali zambiri zoti ziphunziridwe zokhudza nthawi iyi yakuzindikira ndi kukhala kumbali yake. Ndipo sizokhazi. Pomwe m’mikwamba yochuluka kuyesetsa kusonkhera ku ntchito zachitukuko kuli m’ndime zake zoyambilira, Mabungwe Auzimu Akulu, mothandizidwa bwino ndi Alangizi, akuyetsetsa kuphunzira zambiri momwe kuyetsetsa kumeneku kukutulukira kuchokera mu ndondomeko yomanga-mbumba. Zokambirana zokhuza ubwino wachitukuko chakuthupi cha anthu zikufukulidwa m’magulu am’maŵanja ndi mbumba, pomwe abwenzi akupezanso njira zomwe angatengere mbali m’zokambirana zatanthauzo zomwe zikuyamba kutambasuka m’madera owazungulira.

Pa zonse zimene tafotokoza, ntchito za achinyamata zikuwala mochititsa chidwi. Posakhala ongolandira chabe zotsatira—kaya zabwino kapena ayi—iwo awonetsa kuti ndi atenga-mbali a Pulani olimba mtima ndi ozindikira. Kumene mbumba yawaona iwowa mu chilinganizo ichi ndikuyika njira zowapititsira chitsogolo, achinyamatawa awonetsa kuchilimika kwawo. Iwo akuphunzitsa Chipembedzo kwa anzawo ndikupanga kutumikira kukhala maziko a maubwenzi a tanthauzo. Nthawi zambiri, kutumikira monga uku kukumakhala kuphunzitsa iwo amene ali achichepere kwaiwo—kuwapatsa iwo osati maphunziro akuthupi ndi kuuzimu kokha, komanso kuwathandizira pa maphunziro awo akusukulunso. Odzozedwa ndi udindo wopatulika wolimbitsa ndondomeko yainsitichuti, achinyamata achiBahá’í akukwanilitsa ziyembekezo zathu.

Kuyetsetsa konseku kukuchitikira mu dziko lampungwe-pungweli. Kuli konse kwavomerezeka kuti nsichi zadziko lapansi zagweduka ndipo sizingathenso kuchirikiza zosowekera za mtundu wa anthu tsopano. Zambiri zimene zimaoneka ngati zotsimikizika ndi zosatekeseka tsopano zikukayikitsa, ndipo zotsatira zake zikubweretsa kufunitsitsa kokhala ndi masomphenya amodzi. Mavume ovomereza umodzi, kukhala ndi mwayi ofanana, komanso chilungamo zikuonetsa kuchuluka kwa anthu omwe akufunira izi madera awo. Inde, sizodabwitsa kwawotsatira wa Wokongola Wodalitsika kuti mitima ifunitsitse mfundo zauzimu zimene Iye anaziphunzitsa. Ndichochititsa chidwi kuti m’chaka chimene mtundu wa anthu uli ndi chiyembekezo chopitira limodzi chitsogolo sikokayikitsayi, kuwala kwa Chipembedzo kwathwanima m’misonkhano yoposa mazana khumi (10,000) komwe anthu pafupi-fupi chikwi chimodzi ndi theka (1,500,000) amazukuta njira zopititsira mtsogolo mfundozi. Masomphenya ndilangizo la Bahá’u’lláh kumtundu waanthu kugwira ntchito mu umodzi wa ubwino wadziko lapansi, linali phata limene mbali zosiyana-siyana zadera zinasonkhanira mwachidwi—n’chifukwa chake, momwe wafotokozera ‘Abdu’l-Bahá, “mbumba ina ili yonse padziko lapansi ikupeza kuzindikira mu Ziphunzitso izi Zoyera kwamasomphenya ake apamwamba.” Anthu ena akufuna kwabwino poyambilira akhoza kuyitanidwira kumbumba yachiBaha’i ngati kumalo komwe angapeze chitetezo, mthunzi kudziko la tsankho ndi laulumali. Kuposera apa, zomwe akumapeza ndimizimu yaubwenzi yomwe ikugwilira ntchito limodzi kumanga dziko latsopano.

Zambiri zikanatha kulembedwa zokhuza kufalikira kwamisonkhano, mphamvu zapamwamba zomwe inapereka ku Pulani yatsopano, kapena chikondwelero chapansi pa mtima ndikuchilimika komwe inatulutsa mwaiwo amene anakhalanawo pa misonkhanoyo. Koma ndimawu ochepa awa tifuna kupereka chidwi chathu kuchimene chinaonedwa pa kupita mtsogolo kwa Chipembedzo. Inali kalilore wambumba yachiBahá’í imene imaona ubale, osati kusiyana. Ichi chinapangitsa ntchito yozukuta Pulani ya Zaka Zisanu ndi Zinayi kukhala yosavuta pamisonkhano imene anthu onse anali olandiridwa. Abwenzi analingalira zotsatira za Pulaniyi kumadera awo osati ndi mawanja awo okha ayi koma limodzi ndi atsogoleri akudera ndi enanso am’maudindo. Kubweretsa pamodzi anthu ochuluka kunapezetsa mwayi wokambirana mosinthika pankhani zakupita patsogolo kuzauzimu ndi zakuthupi, zimene zikutambasuka padziko lonse. Kusonkhera kwapadera kumene misonkhano imeneyi– imene onse anali olandiridwa, yosuntha komanso yacholinga–kungabweretse kachitidwe kotambasuka kopita m’tsogolo kwambumba mu mkwamba ndiphunziro lalikulu kuzikhadzikitso zachiBahá’í kuti ziringalire mtsogolo muno.

Ndipo tsopano mbumba yaokhulupirika ikulowa m’chaka chachiwiri cha Pulani ndikaganizidwe katsopano ndi kamvetsedwe kozama pa kufunikira kwachimene akuyenera kukwaniritsa. M’mene ntchito zosiyana-siyana zimaonekera poziyang’anira mphamvu zomanga dera zomwe zimatulutsa! Kutambasuka kwa masomphenya uku kukulora ntchito yopitilira kuti iwoneke kwambiri kusiyana ndi nchito yapayokha yakutumikira kapenanso ngati pongotolera chiwerengero. Dera ndi dera, ntchito zomwe zikuchitika zikuvumbula gulu la anthu lomwe likuphunzira kutenga udindo wochuluka kufufuza njira yachitukuko chawo chomwe.

Zotsatira zakusinthika kuuzimu komanso kuthupi zikuoneka zokha m’moyo waanthu munjira zosiyana-siyana. Mu m’ndandanda wa Mapulani apitawo, zolinga zimaonekeratu mu kupititsa patsogolo kwamaphunziro auzimu ndi kupembedza kwapamodzi. Mu m’ndandanda watsopano wa Mapulani, chidwi chowonjezereka chifunika chiperekedwe kundondomeko zina zimene zikufunika pakutukula moyo wambumba—mwachitsanzo, popititsa patsogolo nkhani zaumoyo waonse, kuteteza zachilengedwe, komanso kuchilimika pa mphamvu zamaluso. Chimene chikufunika kumbali zonse zowonjezera zaubwino wambumba kuti zipite patsogolo ndi, indetu, kuthekera kopanga kuphunzira kwandondomeko m’mbali zonsezi—kuthekera kumene kukutsamira pakuphunzira kochokera mu Ziphunzitso ndi kunkhokwe zanzeru za anthu zopezeka kuchokera ku ukadaulo wasayansi. Pomwe kuthekera uku kukukula, zambirizi zidzakwaniritsidwa m’zaka zomwe zikubwerazi.

Masomphenya awa otambasuka, omanga dera ali ndizotsatira zapatali. Mbumba ili yonse ili panjira yakeyake yokwaniritsa ichi. Koma kupita patsogolo kwa malo amodzi nthawi zambiri kumakhala ndi zina zofanana ndikupita patsogolo kwa malo ena. Chinthu chimodzi ndi chakuti, pomwe kuthekera kukuonjezereka ndipo mphamvu zambumba yadera kapena dziko zikuchulukira, kenako, m’kupita kwa nthawi, kufunikira kokhala ndi Nyumba Zopembedzeramo (Mashriqu’l-Adhkár), zomwe tinakamba kale mu uthenga wathu wa Riziwani 2012, zidzayamba kukwaniritsidwa. Momwe tinafotokozera mu uthenga wathu kwa inu wa Riziwani yathayi, nthawi ndi nthawi tidzisankha malo kumene Kachisi wachiBaha’i akuyenera kumangidwa. Ndife okondwa kulengeza, panthawi ino, kukhazikitsidwa kwa Nyumba Yopembedzeramo ku Kanchanpur, ku Nepal, ndiku Mwinilunga, ku Zambia. Kuwonjezera apa, tikulengezanso kuti Nyumba Yopembedzera yam’dziko imangidwe ku Canada, kudera lowandikana ndikomwe kuli likulu la Bungwe Lauzimu kuToronto. Ntchito zimenezi, ndizina zomwe zichitike mtsogolo muno, zizapindula ndithandizo loperekedwa ku Thumba la Nyumba Zopembedzera lomwe abwenzi padziko lonse amasonkhera.

Ochuluka ndi madalitso amene Ambuye wopereka ndi wachifundo wasankha kupereka kwa okondedwa Ake. Kwachiyero ndikuyitana, kukwezeka ndiwo masomphenya. Yofunikira kwambiri ndinthawi imene tonse tayitanidwa kuti titumikire. Kuchokera pansi pamtima, choncho, ndimapemphero amene, m’malo mwanu ndikuyesetsa kwanu kosatopa, tikupempherani pa Mapazi aBahá’u’lláh.

 

Windows / Mac