*Amene akufuna kupempherayo, asambe manja ake, ndipo pamene ali kusamba, anene kuti:
Limbikitsani dzanja langa. O Mulungu wanga, kuti ligwire Bukhu Lanu ndi chilimbiko chomwe makamu a dziko lapansi sadzakhala ndi mphamvu kuligonjetsa. Litchinjirizeni tsono, kuti lisadudukire mchilichonse chomwe sichailo. Ndithudi, Inu muli Wanyonga, Wamphamvu Zopambana.
*Ndipo pamene akusukusula nkhope yake iye anene kuti:
Ndatembenukira nkhope yanga kwa Inu, O Ambuye wanga! Iwalitseni ndi kuunika kwa nkhope Yanu. Itetezeni, chomwecho, posatembenukira kwa wina koma
Inu.
*Tsopano ayimilire ndipo ayang’ane ku Qiblih (ku Bahji, Akka), iye anene kuti:
Mulungu achitira umboni kuti kulibe Mulungu wina koma Iye. Maufumu a Chibumbulutso ndi chilengedwe ndi Ake. Iye, muchoonadi, wabvumbulutsa Iye Amene adayankhula pa Sinai, amene kubzolera mwa Iye Dangaliro lopambana lawalitsidwa, ndipo Mtengo wa Loti umene paseri pake palibe podzera wayankhula, ndipo kubzolera mwa Iye chiitano chalengezedwa kwa onse amene ali m’mwamba ndi padziko lapansi: “Taonani Mwinizonse wabwera. Dziko lapansi ndi kumwamba, ulemelero ndi ulamuliro ndi wa Mulungu, Ambuye wa anthu onse, ndi Mwini wa za m’mwambamo ndi pansi pano!”
*Tsopano Iye, aweramira pansi, manja ali pa maondo ndi kunena kuti:
Wokwezeka Ndinu pamwamba pa chitamando changa ndi chitamado cha wina aliyense pambali panga, opitirira chifotokozo changa ndi chifotokozo cha onse amene ali kumwamba ndi onse amene ali pa dziko lapansi!
*Tsopano iye ayimirire atatambasula manja ake zikato zitapenya kumwamba molunjika nkhope, ndi kunena kuti:
Musamukhumudwitse, O Mulungu wanga, Iye amene, ndi zala zodandaula, wakakamira ku mpindiro wa chifundo Chanu ndi chisomo Chanu, O Inu Amene mwa iwo amene alangiza Chifundo Chopambana!
*Ndipo iye akhazikike pansi, ndi kunena kuti:
Ndichitira umboni ku umodzi Wanu ndi chiphatikizo Chanu, ndi kuti Inu Mulungu, ndipo kuti kulibenso Mulungu wina pambali Panu, Inu, ndithudi, mwaulula Chipembedzo Chanu, mwakwaniritsa Pangano Lanu, ndi kutsegulitsa chitseko cha chisomo Chanu kwa onse amene akhala kumwamba ndi dziko lapansi. Dalitso la mtendere, malonje ndi ulemelero, zikhale pa okondedwa Anu, amene zosintha ndiponso mwayi wa dziko lapansi sizidawalepheretse kutembenukira kwa Inu, ndipo amene adapereka zawo zonse, m’chiyembekezo chokapeza chijacho chimene chilli ndi Inu. Inu zedi, muli Wokhululukira-khululukirabe, Wachaulere Chonse.
*(Ndipo ngati wina aliyense atasankha m’malo mwa ndime yayitali atangonena mawu awa: “Mulungu achitira umboni kuti kulibe Mulungu wina koma Iye, Wothandiza Patsoka, Wodzidalira Yekha,” ndipokwanira. Chimodzimodzi ndipokwaniranso ngati iyeyo atakhazikika pansi asankhe kunena mawu awa: “Ndichitira umboni ku umodzi Wanu ndi chiphatikizo Chanu, ndipo kuti Inu Ndinu Mulungu, ndi kuti kulibe
Mulungu wina pambali Panu.”)
- Bahá'u'lláh